Mafoni anali osaswekwa — Mitaye


Img 20260929 Wa0005- Malawi24
…watsutsa umboni wa Muwanga

Pomwe kusaka mayankho pa ngozi ya ndege kukupitirira, usiku wapitawu kwatuluka umboni wina omwe wabweretsaso mafunso. Mboni ina yati inapeza mafoni awiri omwe anali osaswekwa.

Izi ndi malingana ndi a Glinton Mitaye omwe anali wachiwiri kwa mkulu wa apolisi mchigawo cha kumpoto omwe anawonekera ku komiti yomwe ikufufuza za ngozi ya ndege pa 10 June 2024 yomwe idapha a Saulos Chilima ndi ena 8.

Mitaye adauza komitiyi kuti iwo anapeza lamya zam’manja ziwiri pafupi ndi thupi la malemu Saulos Chilima, ndipo wati iye anakhulupira kuti zinali za yemwe anali wachiwiri kwa mtsogoleri wa dzikoyo.

Chomwe chadabwitsa anthu ochuluka ndichoti a Mitaye ati lamyazo zinali zosasweka paliponse.

“Ndinapeza ma foni awiri pafupi ndi pomwe panali thupi la a Vice President ndipo nakhulupilira kuti atha kukhala awo. Analibe ma crack aliwonse, anali bwino bwino. Nde ntawatenga mnawapatsira a Mwamande a CID kuti asunge pabwino,” watelo Mitaye.

Iye wati lamyazi zinangopakika fumbi ndi dothi pang’ono koma chilichonse chimaoneka chinali mchimake.

Izi zikusemphana ndi umboni omwe anapereka mkazi wa malemu Chilima, Mary yemwe m’mbuyomu adauza komitiyi kuti adapatsidwa foni zoswekwa.

Kuwonjezera apo, Mitaye watsutsanso zomwe ananena Akis Muwanga yemwe anali mkulu otsogolera ntchito ku polisi, yemwe muumboni wake anati anachita kuunika ndi tochi kuti apeze matupi ena.

“Ine ndalumbira, sindinganene zomwe sinazione kapena zomwe sinave, palibe yemwe anayatsa tochi nthawi yomwe timapeza matupi,” wateloso Mitaye.

Iwo ati a Muwanga ataperekera umboni umenewu, awiri mwa anthu omwe anayambilira kufika pamalopa anawaimbira lamya kaamba koti nawonso anadabwa ndizomwe a Muwanga adanena.

Kumbali ya zithuzi za ngozi, iwo ati ankatola zithunzi pa malo a ngoziwa kuti asunge ma umboni ena monga amachitira nthawi zonse, koma a Colonel Julius Mdokhwe adawaletsa mopanda ulemu.

A Mitaye ati pamayenera kukhala kukambirana kwabwino pakati pa adindo akuluakulu a nthambi ziwirizi, ndipo anali odabwa kuti a nthambi ya MDF ndiomwe amkatenga zithunzi.

Iwo ati pa zithunzi zoswa mtima zomwe zinayenda mu masamba a mchezo palibe chomwe chinajambulidwa ndi iwo, komanso sakanakwanitsa kutulutsa zithunzi mosayenera potengera ntchito yawo.

Commissioner Mitaye anatsindika kuti panalibe kulumikizana kwabwino pakati pa asirikali a Nkhondo ndi aPolisi.

Iwo anati samagwirizana ndi kaganizidwe koti asilikali a MDF ndiomwe ankatsogolera ntchito yofunafuna ndegeyi, kaamba koti apolisi ankachita chilichonse popanda kutsogoleredwa ndi asilikali a MDF wa.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.

Discover more from Malawi24

Subscribe now to keep reading and get access to the full archive.

Continue reading