Mulungu iphani onse akufuna kubera aMalawi — Kamangila


Malawi activist Alexious Kamangila linked to Amaryllis Hotel inquiry and corruption allegations

Ngati muli mgulu la anthu omwe akudyera masuku pamutu a Malawi, mkutheka muli ndi masiku owerengeka pomwe woyimirira anthu pamirandu, Alexious Kamangila wapempha Mulungu kuti akukantheni.

Kamangila yemwe amadziwika kwambiri ndi kudana ndi mchitidwe wa katangale wapempha Mulungu kuti aphe anthu onse omwe akuba ndalama za aMalawi.

Iye wati aMalawi pawokha sakukwanitsa kukwiya ndi m’mene zinthu zikuyendera maka momwe atsogoleri ena akudyera ndalama za aMalawi komanso chinyengo chomwe chafika povuta.

Polankhula mu kanema wakewa pompopompo Lamulungu, Kamangira wati zinthu zambiri aMalawi amangokwanitsa kukhudzika kokha ndipo zimathera pomwepo opanda kuchitapo kanthu.

Iye anapereka zitsanzo zingapo kuphatikiza, zomwe zinachitika mu mzinda wa Lilongwe komwe anthu anamwa madzi a zitosi za anthu koma sizinawone mathero ake ndipo ena anayendetsapo chinyengo.

Kamangila wati aMalawi akuseweredwa kwambiri, mwachitsanzo ndi ndalama zoposa 700 million kwacha zasowa ku nthambi yosunga ndi kusamala Mafuta ya National Oil Company of Malawi NOCMA zomwe wati anthu azigawanako.

Apo ndi pomwe wapempha Mulungu kuti ngati anthu ofuna kubera aMalawi atafune kupitilira ndi khalidwe lawo Mulungu angowapha ndi kuwamaliza.

“Ngati amenewa ofuna kubera aMalawi atafune kumapitilira kuba, ingowaphani Atate, amalizeni ndithu, finish them off chifukwa ndinu Mulungu wa chilungamo” anatero a Kamangira mu pemphero lawo.

Iye wati aMalawi asiye kugona kwambiri pa m’mene dziko lawo likuyendera ndipo adzikwiya akawona zinthu sizikuyenda bwino.

Kamangira wagundako kalata yochokera ku nyumba ya Malamulo komanso ku Boma yokambako pa zokhudza kafukufuku wapandera wa katangale m’boma.

Iye anati kafukufuku wa nyumba ya malamulo ndi ofunika kwambiri ndipo odana ndi kafukufukuyu ndekuti akudana ndi aMalawi.

Pakali pano nyumba ya malamulo yayamba yayimitsa kaye chilinganozo chake chokhazikitsa ma komiti 12 ofuna kufufuza za katangale ndi kusayenda bwino kwa zinthu m’boma ndi nthambi za Boma potsatira chiletso cha Ku bwalo la milandu chomwe a Austin Mkoka anatenga.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.

Discover more from Malawi24

Subscribe now to keep reading and get access to the full archive.

Continue reading