Achinyamata, iwalani za ntchito: Miyala ya mtengo wapatali ya mu dziko muno azikaikonzera ku Ulaya


laborer carrying heavy rocks outdoors

…Ndalama pafupifupi 1 thiliyoni zipita ku Poland kukayamba ntchito yosula miyala ya ku Malawi

Pamene sukulu za ukachenjede mu dziko muno zili pakalapakala kusula akatswiri pa ntchito za migodi, zadziwika kuti ambiri mwa iwo atha kukhala chabe malova ochezerera Tikitoko ndi Fesibukhu. Za ntchito za migodi asazilingalire kwenikweni chifukwa ngakhale migodi imeneyi ili mu dziko muno, kwenikweni kumene ikapereke ntchito ndi kwa anthu a ku ulaya ndi Amerika.

Malinga ndi bungwe loona za chuma ndi chitukuko la mu dziko la Amerika lotchedwa United States International Development Finance Corporation (USIDFC), pali chikonzero choti miyala ya mtengo wapatali imene izikumbidwa mu boma la Phalombe izichotsedwa mu dziko muno ndipo izikasulidwa ku dziko la Poland.

construction over rocks near forest
Migodi ipite, umphawi utsale (Photo: ArtHouse Studio/Pexels.com

Bungweli lati fakitale yosula miyala imeneyi imangidwa mu dziko la Poland pa mtengo wa ndalama zoposera 200 miliyoni ya Amereka imene kuisintha pa mtengo umene anthu akugulitsilana ndalamayi ku Malawi kuno ukumaposa 800 biliyoni Kwacha. Polemba pa tsamba lawo la intaneti, a bungwe la USIDFC ati miyala yomwe izikumbidwa mu dziko muno izitengedwa kupita ku Mazambiki isanapochezedwe pa ulendo wa ku fakitale ya ndalama za nkhani nkhani ngati iyi.

Pothirira ndemanga pa chilinganizochi, katswiri wina wa zamigodi amene anakana kutchulidwa anadabwa ndi dongosolo lotere ponena kuti ntchito zikuluzikulu ndi zofunika ndizo zimene zikukapangidwa komwe kuli fakitaleyi. Iye anaunikira kuti izi zikutanthauza kuti a Malawi phindu lomwe angapeze ndi ntchito za kalavulagaga chabe.

“Ndi zodabwitsa kwambiri chifukwa apa ndiye kuti ntchito zomwe zikanatha kusintha moyo wa a Malawi komanso kupindulira chuma cha dziko lino zikupita ku Poland. Ndi zoona kuti a Malawi ena apezapo ntchito koma kwambiri ikhala yokumba, yolambula miseu ndi zina zotero. Ntchito zonse zotsuka bwino miyala imeneyi zomwe ndi zapamwamba komanso zolipira bwino ndiye kuti basitu zikhala ndi azungu,” anatero mkuluyu.

Pofunsidwa ngati Malawi ili ndi kuthekera kosula miyala imeneyi, iye ananenetsa kuti ukadaulo ulipo.

“Ma Yunivesite athu akusula anthu aluso limeneli amene ambiri tsopano angokhala mmakomomu, uwu unali mwayi oti alembedwe ntchito ndipo athandize ku chitukuko cha chuma,” iye anatelo ndipo anatchulapo sukulu monga za Malawi University of Business and Applied Sciences (MUBAS) zomwe zakhala zikusula achinyamata pa nkhani za migodi.

Atangolowa kumene m’boma mu chaka cha 2025, a Mutharika adalamula kuti miyala yonse ya mtengo wa patali izisulidwa mu dziko muno koma zikuoneka kuti lamulo lawo silinamveredwe ndi komwe pa nkhani yokhudzana ndi mgodi wa Songwe omwe ukhale boma la Phalombe. Mgodiwu uli m’manja mwa kampane ya Mkango minerals.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.

Discover more from Malawi24

Subscribe now to keep reading and get access to the full archive.

Continue reading