Akwaya 15 ali mchipatala atadya chakudya chokaikitsa


Ambulance- Malawi24

Mamembala a kwaya khumi ndi asanu (15) mumpingo wa Chikuyu CCAP omwe uli pansi pa Milala Presbytery ku Mzimba athamangira nawo kuchipatala chaboma atadya chakudya chomwe akuchikayikira kuti chinali ndi poyizoni.

Group Village Headman German Mahowe komanso wapampando wa Vesitere ya Mpingo wa Chikuyu CCAP, a Richard Mhoni ati anthuwa akukayikira chakudya chomwe anadya pa nthawi ya chikondwerero cha kwaya chomwe chinachitika Lamulungu.

Malingana ndi a Mahowe, mamembalawa anayamba kumva zizindikiro zosakhala bwino Lolemba komanso Lachiwiri monga kuphwanya kwamutu, kufooka kwa miyendo, komanso kutsegula m’mimba.

Ataona izi, mamembalawa anafuna kupeza thandizo lachipatala ataona kuti zinthu sizikusintha.

Mkulu woona zachipata m’boma la Mzimba, a Dr Angelo Mwaungulu anatsimikiza kuti kuti chipatalachi chalandira anthu 15 omwe akukhudzidwa kuti adya chakudya chokayikitsachi.

Apa a Mwaungulu anati akuluakulu azachipatala akuchita kafukufuku pofuna kudziwa ngati mamembalawa anadyadi chakudya chomwe akuchikayira kuti chili ndi poyizoni.

Sponsored

Join the conversation — share your thoughts on this story

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.

Discover more from Malawi24

Subscribe now to keep reading and get access to the full archive.

Continue reading