Sing’anga wafa atalumidwa ndi njoka yake yomwe


Machinga Singanga Njoka- Malawi24

Tsoka likalimba amakuluma ndi wako yemwe! Sing’anga wazaka 46 wafa kudera la Mbanira m’boma la Machinga njoka yake yomwe amagwiritsa ntchito pochita zamatsenga itamuluma.

Wofalitsa nkhani za polisi m’boma la Machinga Western Kansire, wati malemu Steve Moyenda wakumana ndi tsokali pomwe anachita matama achule odumpha popanda dzenje kumuwonetsa sing’anga mzake njoka yakeyi.

Moyenda atabwezeretsa njoka yakeyi m’malo mwake, posakhalitsa adangova njii! Njokayo yamuluma chala chake ku dzanja la manzere.

“Ase ndithandize yandiluma,” adakuwa Moyenda kumuuza sing’anga nzakeyo.

Pogwiritsa ntchito mwambi woti anjinga adziwana pobwerekana pampu, sing’anga winayo adakangalika kutulutsa mankhwala azitsamba kuti amuthandize dotolo nzakeyo.

Atawona kuti using’anga wakanika, ndipomwe adaganiza zomutengera nzakeyo kuchipatala cha Ntholowa m’boma lomweli, koma madzi adali atachita kale katondo.

Pakadali pano, zotsatira za chipatala zatsimikiza kuti sing’anga Moyenda adafa kaamba ka poizoni wa njoka.

Join the conversation — share your thoughts on this story

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.

Discover more from Malawi24

Subscribe now to keep reading and get access to the full archive.

Continue reading