Ndikuganiza zakumwa mankhwala ngati sitikwatilana – Promise


Pro- Malawi24

Kutsatira chigamulo cha polisi ya Lobi m’boma la Dedza, kuti mnyamata wina alipire ndalama yokwana K2.5 miliyoni kamba kochita zachikondi ndi mtsikana yemwe otchedwa Promise, msungwanayu wati ali ndi malingaliro omwa mankhwala ngati sakwatirana ndi njondayi.

Malingana ndi Promise, masiku apitawa bwezi lake linanjatidwa poliganizira kuti limakoza zomukwatira komaso limachita naye zadama.

Iye wati ngakhale anatsutsa zoti zaka zake ndizosayenera kulowa m’banja, koma amalume ake anatemetsa nkhwangwa pamwala ndikumangitsa njondayo, yomwe sanaitchule dzina.

“Ndinabadwa mu 2007 ndipo kufika lero ndili ndi zaka 19 mmene mukuwonera chiphaso changa cha umzika” anatero Promise.

Msungwanayu wati ndiwokhumudwa kwambiri kuti akumulekanitsa ndi munthu yemwe amamvana naye kwambiri.

Iye anapitiriza ndikuwonetsa kusakondwa ndi ndalama yomwe analipiritsa bwezi lakeli, ponena kuti analipira pa mulandu wa bodza.

“Ndikufunitsitsa kuti ineyo ndi iyeyo titakhala malo amodzi, ndichifukwa chake ndikuganiza kuti akangondisiya ndimwa mankhwala” anapitiriza motero.

Promise wati akufunitsitsa akufuna kwabwino alowerere ndikuthandiza kuti chilungamo pa ganizo lake lofuna kukwatira komaso pa ndalama zomwe analipira bwezi lake chidziwike.

Msungwanayu wati analephera kupitiriza maphunziro ake a sekondare pomwe makolo anamunyanyala ndipo pano amangokhala.

Izi zabweretsa zokamba pakati pa anthu pomwe ena alangiza mtsikanayu kuti abwerere kusukulu pomwe ena ati pakufunika atsikana ngati awa, omwe angamateteze ufulu wa amuna ambiri omwe akumalowa ku ndende koma osalakwa.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.

Discover more from Malawi24

Subscribe now to keep reading and get access to the full archive.

Continue reading