Othandizira kuphunzitsa timu ya Kamuzu Barracks, Joseph Chilapondwa, wapempha akuluakulu oyendetsa masewero a mpira wa miyendo m’dziko muno kuti awunikire mwachangu, ndalama zisanawononge mpikisano wa chaka chino.
Chilapondwa wayankhula izi lero pomwe timu yake yagonja m’manja mwa LUANAR Mitundu Baptist, ndichigoli chokhacho chobwera nthawi yowonjezera kuchokera kwa Emmanuel Chikadza yemwe anamwetsa kudzera pa penote.
Iye anati ma timu onse anasewera bwino koma oyimbira ndiyemwe sanali bwino m’masewerowa zomwe zapangitsa kuti asirikaliwa agonje pa bwalo la Dedza.
“Chimene ndinganene ndichoti ndalama ziwononga mpira wa chaka chino, ofunika akuluakulu awunikire bwino” anatero Chilapondwa.
Timu ya KB tsopano yagonja masewero onse awiri chiyambire FDH Premiership ya chaka chino, koma Chilapondwa watu otsatira KB asadandaule kamba koti posachedwapa timuyi inyamuka ndipo zikhala zovuta kuti ma timu ena ayiyimitse.
Mphunzitsi wa Mitundu Baptist Oscar Kaunda wati ndiwokondwa kuti timu yachita bwino ndikutenga ma point atatu oyamba chaka chino.
Kaunda wati nthawi zina osewera ake amachita mantha potengera kuti amasewera ndi timu yachisilikali, koma wati apitilira kuwalimbikitsa pomwe masewero akupitilira.
Tsopano Mitundu Baptist ili ndi mapoint anayi pamasewero awiri, kutsatira kulepherana kwawo ndi MAFCO sabata yatha.









