Osewera akulephera udindo wawo- Chatama


Malawi football coach practicing drills on a sunny day.

M’phunzitsi wa timu ya Ekhaya, Enos Chatama, wati china mwa zifukwa zomwe timu yake sinayambe bwino m’masewero a FDH Premiership ndikulephera kutenga udindo kwa osewera ake.

Chatama yemwe amayankhula timu yake italepherana ndi Red Lions pogoletsana chigoli chimodzi kwa chimodzi pa bwalo la Mpira mu mzinda wa Blantyre, anawonetsa kusakondwa maka ndim’mene timu yake ikuchitira kuti iteteze komaso kupeza chigoli.

Ekhaya inali yoyamba kugoletsa kudzera mwa Blessings Malinda m’chigawo choyamba koma Red Lions inabweza m’chigawo chachiwiri kudzera mwa Fred Banda.

Malingana ndi Chatama, ngati mphunzitsi anapereka upangiri wabwino omwe ukanathandiza timu yake koma osewera sanagwiritse ntchito.

“Ngati timu ikumapatsirana mpaka kukafika ku golo la adani koma tikulephera kupambana, taphonya kwambiri komaso tachinyitsa chigoli chomwe tikanatha kupewa ndiye vuto kwenikweni ndiloti osewera akulephera kutenga udindo” anatero Chatama.

Ngakhale zili chonchi, Chatama wati sakutaya mtima chifukwa nthawi ifika yomwe Ekhaya iyambenso kuchita bwino.

Awa anali masewero achiwiri a Ekhaya yomwe inagula osewera ambiri patsogolo pa chaka chino cha mpira ndipo yakwanitsa kutolera point imodzi pamasewerowa.

Malumbo Mkandawire yemwe akuphunzitsa Red Lions wati point yomwe atolera lero iwathandiza kuchita bwino mmasewero akutsogoloku.

Red Lions tsopano ili ndima point awiri pa maseweronso awiri.

Discover more from Malawi24

Subscribe now to keep reading and get access to the full archive.

Continue reading