Miyoyo yambiri ipululuka mukasiya kuthandiza dziko la South Africa – UNAids yauza America
Pamene dziko la South Africa liri ndi anthu oposera 8 million omwe ali ndi kachilombo koyambiya Edzi ka HIV, bungwe la UNAids lapempha dziko la America kuti lisasiye kuthandiza dziko la South Africa pa nkhani zothana ndi kachilomboka kaamba koti akatero miyoyo yambiri ipululuka.
Polankhulapo pankhani yoti dziko la America lisiya kuthandiza dziko la South Africa pothana ndi matendawa, mkulu wa UNAids Winnie Byanyima wapempha utsogoleri wa dziko la America kudzera mwa a Donald Trump kuti aganizenso pankhani yofuna kusiya kuthandiza dzikoli kaamba koti izi ziika pachiopsezo miyoyo yambiri.
Byanyima wati anthu ambiri ankhonza kutaya miyoyo yawo makamaka amene alibe kuthekera kopeza zinthu zozitetezera ku nthendayi ndipo izinso zichititsa kuti zonse zomwe achita m’mbuyomu pofuna kuthana ndi nthendayi zikhale zosapindula.
Koma dziko la South Africa litamva za ganizo lomwe dziko la America lakonza pa nkhani yosiya kuthandiza dzikoli, ilo lati lidaika kale ndondomeko zofuna kuthana ndi nthendayi ndipo silidalira dziko la America pa nkhaniyi.
Mtsogoleri wa dziko la America, Donald Trump wakhala akudzudzula dziko la South Africa kaamba ka mchitidwe wake ozunza anthu achizungu mdzikolo, ndipo mwa zina, ndi zomwe zapangitsa dziko la America kusiya kuthandiza dzikoli. Izi zili chomwechi, dziko la South Africa lakhala likukanitsitsa kwa mtu wa galu za mchitidwewu.
M’mbuyomu dziko la America lakhala likuthandiza dziko la South Africa pankhani zothana ndi matenda a Edzi kudzera mu ndondomeko ya President’s Emergency Fund for Aids Relief (Pepfar), ndipo America yakhaka ikupeleka thandizoli ndi pafupifupi 17%.









