Mfumu yaikulu Kachenga yamwalira


Malawi traditional leader

Mfumu yaikulu Kachenga ya m’boma la Balaka yamwalira.

Bwanamkubwa wa boma la Balaka a Tamanya Harawa ndiwo atsimikiza izi mu kalata yomwe asainira.

A Harawa ati mfumu Kachenga yamwalira lero masana akulandira chithandizo cha mankhwala pa chipatala cha Zomba Central.

Mwambo oika m’manda thupi la  malemu  Kachenga, omwe dzina lawo ndi Mary Saidi, ulengezedwabe.

Anabadwa pa 22 July 1984 ndipo asiya ana asanu ndi zidzukulu zitatu.

Discover more from Malawi24

Subscribe now to keep reading and get access to the full archive.

Continue reading