Wophunzira wa folomu 3, pasukulu ya sekondale ya Mulanje Mission m’boma la Mulanje, akusimba lokona pomwe wapata mphoto ya K5 miliyoni, mu mpikisano wa Airtel Money Tola.
Yamikani Lihoma wa zaka 20, anali ndi chimwemwe chodzaza tsaya pamene akuluakulu a Airtel Money anamuimbira lamya kumudziwitsa kuti ndi m’modzi mwa opambana mphotoyi mu sabata yachitatu ya mpikisanowu.
“Chimwemwe changa ndichachikulu kuti ndapambana mphoto imeneyi” anatero Lihoma. “Ndalamayi indithandiza ku maphunziro kamba koti ndigula zofunikira ku sukulu”.
Lihoma watiso kupatula kumuthandiza kumbali ya maphunziro, ndalamayi imuthandizanso kuyamba bizinesi.
Kupatula Lihoma, ena omwe apata mphoto ya K5 miliyoni ndi a Kenneth Simfukwe aku Chitipa komaso a Chisomo Maloya aku Lunzu munzinda wa Blantyre.
A Simfukwe komaso Maloya yemwe amagulitsa tomato, anyezi komaso matemba, ati ndalamayi iwathandiza kugula malo ndikumangira nyumba.
Kupatula atatuwa, anthu ena okwana 300 apambana ndalama zokwana K50,000 aliyense.
“Ndife okondwa kuti kuyambira masabata atha omwe tinayamba mpikisanowu, akupambana anthu osiyanasiyana zochita,” watelo mkulu wazamalonda ku Airtel Money, Joshua Sichinga.
Kampaniyi yati pofika pano yakwanitsa kupereka ndalama zokwana 90 miliyoni kwacha kwa anthu omwe apambana ndalama.
Kuti munthu apambane mu mpikisanowu omwe ndiwandalama zokwana K600 miliyoni ndipo mphoto yayikulu idzakhala 50 miliyoni kwacha, akuyenera kutumiza ndalama, kugula ma bandulo komaso kulipira ma bilu, zonsezi kudzera pa Airtel Money.