Timu yathu ndiya ana achichepere – Chavula


Timu yathu ndiya ana achichepere - Chavula- Malawi24

Othandizira kuphunzitsa timu ya Ekhaya, Moses Chavula, wati timu yake sinapezebe chipambano mu FDH Premiership yachaka chino kamba koti ndi ya ana achichepere.

Chavula wayankhula izi lero pa bwalo la zamasewero la Civo, timu yake itagonja chigoli chimodzi kwa duu m’manja mwa Civo Service United kudzera mu chigoli chokhacho cha John Dambuleni mu phindi yachi khumi.

“Tingofuna kuwalimbikitsa achinyamata, kuti muone timu yathu ndi ana achichepere kwambiri” anatero Chavvula atafunsidwa chitsogolo cha timu potengera kuti sinapezeko chipambano pamasewero atatu oyambirira chaka chino.

Chavula wati akhala akulimbikitsa osewera ake kamba koti timu ikudutsa mu nyengo yovuta kwambiri.

M’phunzitsiyu watinso ali ndi timu yabwino ndipo akangopeza chipambano choyamba zipangitsa timuyi kuyamba kuchita bwino.

Pokambapo zamasewero a lero, iye wati timu yake inachita bwino kumbali yopeza mipata yambiri m’chigawo chachiwiri koma anadandaula kuti timu sinagwiritse bwino mipata komanso inachinyitsa mwachangu.

Kumbali yake, mphunzitsi wa Civo Service United Abbas Makawa anavomereza kuti timu yake sinasewere bwino koma wati ndi okondwa kuti apeza chipambano.

Zateremu, Civo Service United yabwera pamwamba pa FDH Premiership ndima point 7 pamasewero atatu, pomwe Ekhaya FC nayonso yasewera atatu koma ili pa 14 ndi point imodzi.

Join the conversation — share your thoughts on this story

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.

Discover more from Malawi24

Subscribe now to keep reading and get access to the full archive.

Continue reading