“Ndinyasi”: Sindikudzapikisana nawo pa chisankho cha 2025 — watero Bushiri

Advertisement

…ati iwo si asataniki

…ati iwo sanayambane ndi Mlaka

Mtsogoleri wa mpingo wa ECG Jesus Nation mneneri Shepherd Bushiri wanenetsa kuti iye siwandale ndipo wati sakudzapikisana nawo pa mpando wa utsogoleri wadziko pa chisankho cha mchaka cha 2025.

Bushiri amayankhula izi pomwe amayankhula ndi wailesi ya Times momwe wafotokoza zinthu zambiri zomwe aMalawi akhala akufuna atamva kuchokera kwa iye.

Munkuyankhula kwake iye watsutsa mwantu wagalu mphekesera zomwe zakhala zikuveka mdziko muno kuti mneneriyu akufuna kuyamba ndale.

Iye wati mphekesera zomwe anthu akhala akufalitsa zoti iye akudzaimira pa mpando wa mtsogoleri wa dziko, ndi bodza lamkunkhuniza ndipo wati anthu asazitengere.

Bushiri wati iye sanalotepo za ndale, wati alibe maganizo odzayamba ndale ndipo wati zomwe zikumvekazi ndi “nyasi” zomweso wati cholinga chake ndi kufuna kuipitsa ambiri yake.

Koma poti utsi siumafuka popanda moto mneneriyu wati akuganiza kuti mphekeserazi zikufala kaamba koti iye wakhala akuchita ntchito zachifundo m’dziko muno.

Apa iwo anati nthawi zina anthu amayamba manong’onong’o munthu akakhala akuchita zinthu zina mwa pamwamba komaso mwa utsogoleri.

“Siine wa ndale, sindikupikisana ndi wina aliyese mu 2025. Nditha kuwatsimikizira aMalawi kuti ine si wa ndale ndipo ndale sichibadwidwe changa. Nthawi zina umakhala mlandu kowoneka ngati mtsogoleri, nthawi zina zimene timachita monga ntchito za chifundo zimawapangitsa anthu kuti aziganiza kuti ndine wa ndale.

“Pali kusiyana kwambiri pakuchita ndale ndikukhala mtsogoleri. Nkhani zimenezi zinayamba 2015 pamene ndinathandiza anthu oposa 2 miliyoni ndi chimanga, mu 2018 ndinabweretsa chimanga chotchipa choncho anthu akaona zinthu ngati zimenezo amaona ngati ndine wa ndale. Zomwe zikuvekazi ndi nyasi, ine siwandale,”watelo mneneri Bushiri.

Iwo akanaso kuti anathandizapo chipani cha Malawi Congress komaso otsutsa mphekesera zoti pano akuthandiza ndi ndalama chipani cha Alliance For Democracy (AFORD).

Iwo ayamikira utsogoleri wa a Lazarus Chakwera kuti ukuwalora kumachita ntchito za chifundo pomwe ati muulamuliro wa m’mbuyomu akhala akuletsedwa kumagawa katundu kwa anthu.

“Mukukumbukira kuti inalipo nthawi ina yake yomwe ine sindimaloredwa kuti ndigawe zinthu m’dziko muno, panopa ndikuloredwa nde sindingayambeso kumawawalira a pulezidenti omwewoso,” watelo mneneri Bushiri.

A Bushiri akanitsitsaso zomwe anthu amawanena kuti iwo ndi a sataniki ndipo ati vuto ndiloti aMalawi ambiri akamuona mzawo akupita patsogolo amayamba kumupekera nkhani cholinga abwelele m’mbuyo.

“Mmene ndikuonekeramu, ndikuoneka wazitsamba? Ndimalalikira za Yesu ndipo palibe tsiku ndi limodzi lomwe ine pakamwa panga panatuluka dzina la satana kapena kuwauza anthu kuti amulambire satana.

“Amalawi tiyeni tikondaneni, zomapangirana nsanje ndizachikale. Izi za nsanje zomati wina akalemera kumamunena kuti ndi wasataniki, tisiye. Kunja munthu akamapanga bwino amamuombera mmanja koma kwathu kuno anthu akumagwetsedwa mphwayi,” anateloso Bushiri.

Pantchito yomanga mzinda wawo wa Goshen m’boma Mangochi, mtsogoleri wa ECG wati ndalama za ntchitoyi zikumachokera ku mabizinezi omwe iwo anapanga m’dziko muno komaso kunja.

Munthu wa Mulungu yu, watsotsaso mphekesera yomwe inaveka m’mbuyomu kuti pakati pa iwo ndi oyimba Mlaka Maliro pali mbale wa khoswe ndi mphaka.

Iwo ati ku choka kwa a Maliro mu mpingo mwawo ndi kamba koti pali zinthu zina zomwe a Malirowo sizinawasangalatse zokhudza tchalitchi koma ati pakati pa awiriwa palibe udana uli onse.

“Panachitika nkhani yokhudza akazawo nde analemberedwa kalata kuchokera ku akuluakulu a mpingo osati ine. Ineyo ndi Mlaka Maliro, akazi awo palibe vuto lili lonse, takhala tikukumana, anabwelapo ku ofesi zanga tinacheza bwino bwino,” anatelo a Bushiri.

Follow us on Twitter:

Advertisement