Mnyamata wa zaka 19, Alex Abinala, wadzimangilira atazindikira kuti wabetsa ndalama kwa mbalanyenga zina pa foni.
Malingana ndi wofalitsa nkhani pa polisi ya Luchenza, Baseke Mwale, Abinala analandira uthenga wabodza womudziwitsa kuti walandira ndalama zokwana K785,000 pa Airtel Money yake.
A tsizinamtolewa anamuuza Abinala kuti atumize kaye ndalama zokwana K500,000 ku manambala awiri a TNM ndi Airtel omwe anamupatsa.
Mphuno salota, Abinala anapita kwa ejenti kukatumiza ndalamazo, koma posakhalitsa anazindikira kuti akaunti yake sinalandire ndalama zilizonse komanso kuti uthengawo unali wabodza.
Mwale wati malemuwo anasiya foni yake kwa ejentiyo, akulonjeza kuti abweretsa ndalamazo, koma sanabwererenso.
Ejentiyo anapita kunyumba kwa Abinala kuti akamufunefune koma sanamupeze.
Thupi la Abinala linapezeka masana a tsiku lomwelo.
Lipoti lachipatala lasonyeza kuti Abinala anamwalira chifukwa chobanika, ndipo panalibe zizindikiro zosonyeza kuti wachita kuphedwa.
Alex Abinala, amachokela ku dera la mfumu Nameta, pansi pa Mfumu Yaikulu Ngolongoliwa m’boma la Thyolo.

