Mfuti inalira katatu itangogwa ndege — mboni


Img 20260916 Wa0015- Malawi24

modzi mwa mboni yomwe inawona kugwa kwa ndege yomwe inapha yemwe anali wachiwiri kwa mtsogoleri wadziko, a Saulos Chilima, awuza nyumba yamalamulo kuti anamva kulira kwa mfuti katatu, ndegeyi itangogwa kumene.

Mayi Flora Mkandawire omwe amakhala nyumba zoyandikira ndi phiri la Nthungwa lomwe ndegeyi inagwera, pa tsikuli analawirira mu phiri kukatola nkhuni, koma anabwezedwa ndi anthu ena ovala zachisilikali.

“Anthu awiri ovala zachisilikali atandifusa chomwe ndikupanga ku phiri ndinawauza kuti ndikutola nkhuni ndipo anandibweza, ponena kuti sikololedwa kutero,” watero Mkandawire.

Mayiwa ati atangosiyana ndi anthuwa kuuyatsa ulendo obwelera kwawo, anawona ndege yotuwa yomwe inkawuluka mmusi kulowera mbali yaku Mzuzu.

Iwo ati sipanatenge nthawi, ndipo anawona ndigeyo itatembenuka kubwerera komwe inkachokera kenaka inagwa.

“Ndegeyi itabwerera inayima mmalere mwina kwa mphindi zitatu itatulutsa mateyala kenaka inagwa,” watero Mkandawire.

Mkandawire wati anaganiza zokanena ku polisi koma ali pa njira anakumana ndi mphunzitsi wamkulu wapa sukulu ya Nthungwa yemwe anawapatsa nambala yaku polisi kuti awadziwitse.

Malingana ndi maiwa, wapolisi wamkazi yemwe anayankha lamya atamudziwitsa, anayankha kuti nkhaniyi ayipereka kwa a polisi achigawo chakumpoto, ku Mzuzu.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.

Discover more from Malawi24

Subscribe now to keep reading and get access to the full archive.

Continue reading