Ena akuikira kumbuyo bambo wokumba manda ake


Kalitsiro Kukumbitsa Manda Ake- Malawi24

Pomwe kwa ena ndi mwikho, ambiri maka pa masamba amchezo ati sakuwonapo vuto ndi zomwe ikuchita njonda ina ku Dowa yomwe ikukumbiratu dzenje lomwe anthu ambiri safuna ataliwona.

Faidoni Benamu Kalitsiro wazaka 78, wadodometsa anthu pomwe wayamba ntchito yokumba manda ake m’mudzi wa Makwani m’dera la mfumu yayikulu Dzoole m’bomali.

Benamu Kalitsiro wati ntchito yokumba mandawa ikuyembekezeka kugwiridwa kwa masiku osachepera anayi ndipo wati ikatha ayamba ndondomeko yowaka, kenako kuyamba kusamalira kufikira tsiku lakufa kwake.

Kuwonjezera apo, mkuluyu watinso ndalama ya zakudya zofunikira pa mwambo wa maliro adapereka kale kukomiti ya m’mudzimo, ati pofuna kuti asadzavutitse anthu ena kuphatikizapo abale.

Mbuyomu Benamu Kalitsiro adalengezanso kuti waguliratu bokosi loti adzamuyikemo akadzamwalira lomwe akuti adaligula pa mtengo wa K950,000.

Pothirira ndemanga za nkhaniyi pamasamba amchezo, anthu ambiri ati zomwe wachita mkuluyu sizodabwitsa ponena kuti sizikusiyana ndikudzigulira ndondomeko za inshuransi (funeral policy/life insurance).

“Palibe chachilendo apa, izi zikungofanana ndi life insurance mumakakhomera kuma bungwe ena aja, kungoti iyeyu izizi akuzipangira payekha,” watero Christopher Sk poyikira mlomo za nkhaniyi pa tsamba lina.

Nawo a Mpha Maliba Gama anaphera mphongo ponena sakuwona vuto lili lomse. Gama wati anthu ena akudabwa kaamba koti Benamu Kalitsiro akuigwira yekha ntchitoyi.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.

Discover more from Malawi24

Subscribe now to keep reading and get access to the full archive.

Continue reading