“Tangowapatsa zigoli” watero Ikwanga pomwe Chitipa yafa kwa Wanderers yomwe yapita pamwamba


Fdh Bank Premiership Malawi24

Mphunzitsi wa Chitipa United Kondwa Ikwanga wawonetsa kusakondwa ndimmene timu yake imatchingira kumbuyo pomwe timu yake yagonja ndizigoli zinayi kwa chilowere mmasewero omwe anachitikira pa bwalo la zamasewero la Chitipa mu FDH Premiership. 

Isaac Kaliati, Lameck Mithi ndi Muhammad Sulumba komaso Blessings Joseph chodzibaya yekha, anathandiza Manoma kuti adzibwerera ku Blantyre ndi chipambano.

Atatha masewero, Ikwanga anati: “Zomwe tinakonza kuti tisachinyitse mphindi khumi zoyamba sibwezi titagonja chomchi. Zigoli tachinyitsa anyamata kumangoonera, zigoli zongopereka.”

Kondwa Ikwanga- Malawi24
Kondwa Ikwanga

Komabe Ikwanga anati zomwe zachitikazi ndizomwe zimakhala m’masewero a mpira ndipo wati akawayankhula osewera ake poti ndi ana.

Chitipa United ili pa nambala 13 mu ndandanda wamatimu pomwe yapeza ma point 6 mmaseweroso 6.

Kumbali yake, m’phunzitsi wa Mighty Wanderers, Bob Mpinganjira, anayamika osewera ake popeza chipambano chazigoli zambiri, ngakhale anati sanali masewero ophweka.

Zateremu Manoma apita pamwamba pa matimu onse mu mpikisanowu atasewera masewero 6 tsopano ali ndi mapoint 13 ndipo achotsa Silver Strikers pamwamba yomwe akufanana nayo ma point koma Wanderers ili ndi zigoli zambiri.

Join the conversation — share your thoughts on this story

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.

Discover more from Malawi24

Subscribe now to keep reading and get access to the full archive.

Continue reading