M’phunzitsi wa timu ya Moyale Barracks, Prichard Mwansa, wati wavomereza zotsatira zomwe timu yake yapeza lero ngakhale khumbo lake linali lopeza ma point onse, pamasewero omwe alepherana ndi FCB Nyasa Big Bullets.
M’masewero a FDH Premiership omwe anachitikira pa bwalo la zamasewero la Joyce Chitsulo Lamulungu, Moyale Barracks inachitaya yokhayokha kumapeto pomwe inaloleza George Chaomba kufananitsa mphamvu, itatsogola kwa mphindi pafupifupi 30 kudzera mu chigoli cha Lucky Mkandawire.
“Tasewera mpira wabwino mmasewero onse koma tangolakwitsa pamodzi pomwe wotchinga pagolo wathu analowa mkati ndipo Bullets inagoletsa. Sitinabwere kudzatenga point imodzi, timafuna onse amodzi ndi mmene mpikisano uliri panopa komabe ndi mbali imodzi ya mpira, tibwerera tikakonze” anatero Mwansa.
Atafunsidwa ngati mwina kupha nthawi komanso kukhala ndi osewera ambiri otchinjiriza kumbuyo mu mphindu 30 zomaliza kunathandizira Bullets kubweza, m’phunzitsiyu anavomereza ndipo anati akawalangiza onsewera ake kuti akonze asanabwere masewero ena.
“Timamenya koyenda komaso Bullets ndi imodzi mwa matimu akuluakulu m’dziko muno, nawoso amafuna chipambano. Tinayesetsa kutchinjiriza koma tikabwerera tikuyenera kukawaphunzitsa osewera kuti ulendo wina adzachite bwino.
Zitatha mphindi 90, wothandizira oyimbira anawonjezera mphindi 8 ndipo Bullets inabweza mu mphindi yachisanu, ndipo patadutsa mphindi imodzi katswiri wa Moyale FC Chisomo Chiwanda analandira khadi yofiira atagwiragwira Mike Mkwate.
Zateremu Moyale ili pa nambala 8, masewero 6 ili ndi mapoint okwana 8.









