Mphunzitsi ogwirizira ku timu ya FCB Nyasa Big Bullets, Heston Munthali wati ndiwokhutira ndimmene osewera a timu yake anachitira pa bwalo la zamasewero la Joyce Chitsulo, pomwe timuyi yalepherana ndi Moyale FC mu FDH Premiership.
Lucky Mkandawire anasumbira mu ukonde wa Bullets pa mphindi 54, kuyitsogoza Moyale koma Maulle anabweza mu mphindi yachisanu yowonjezera kudzera mwa George Chaomba kuti matimuwa alepherene.
Atatha masewero, Munthali anati ngakhale timu yake yalephera kutenga ma point onse, koma ndiwokondwa kuti zomwe anawakonzekeretsa osewera zimatheka.
“Masewero anali abwino, koma pang’ono ndakhumudwa chifukwa talephera kugwiritsa ntchito mipata yochuluka yomwe tinapeza make mchigawo choyamba” anatero Munthali
Mphunzitsiyu anapitiriza kunena kuti; “Chigawo chachiwiri mpira umayenda bwino bwino, tinapezaso mipata yambiri komaso sitinachinye. Ndiwayamikire osewera chifukwa zomwe tinakonza zimachitika kupatula kusagwiritsa ntchito mipata”
Heston Munthali anawonetsaso kusakondwa ndichigoli chomwe timu yake yachinyitsa ponena kuti mlingo wa Bullets siwoyenera idzichinyitsa zigoli zochoka pa kona.
Iye wati apitirira kukonza mofooka, maka vuto logoletsa akabwerera kuzokonzekera za timuyi.
Awa anali masewero oyamba a Heston Munthali kutsogolera ngati mphunzitsi wamkulu wa timu, pomwe walowa mmalo mwa Gilbert Chirwa yemwe anachotsedwa ku timuyi.
Pakadali pano Bullets ndiyachisanu ndi chimodzi (6) pa mndandanda wamatimu mu FDH Premiership pomwe yakwanitsa kutolera ma point 10 pamasewero 6.









