Dedza Dynamos yapeza chipambano choyamba


Dedza Dynamos- Malawi24

Patadutsa masewero asanu osagoletsa komanso osapeza chipambano, Goshen City Dedza Dynamos lero yagwiritsa ntchito mwayi osewerera pakwawo pomwe yagonjetsa Kamuzu Barracks chigoli chimodzi kwachilowere.

Zateremu Dynamos yasuntha pa mndandanda wamatimu kuchoka pa nambala 16 kufika pa 15 pomwe inadalira chigoli chokhacho cha Chifuniro Mpinganjira.

M’phunzitsi wa Dedza Alex Ngwira anati chipambanochi ndichofunika kwambiri chifukwa chabwera pa nthawi yabwino pomwe zinthu sizimayenda bwino ku timuyi. 

Iye anati: “Ichi ndichilimbikitso chifukwa timadzikayikira kwambiri kuti tingachinye, tsopano pakhala kudzikhulupirira kuchoka kwa osewera kuti ndizotheka”.

Kumbali ya Kamuzu Barracks, zinthu sizikuyendabe pomwe yatsakamira pa nambala 14 itangotolera ma point okwana anayi okha.

M’phunzitsi wa timuyi Kenwood Nkhoma wati timu yake ikuchita bwino pakaseweredwe koma mwayi ndi omwe akuvuta kuti upezeke.

“Sitinatayike, mipata tikupeza koma anthu asataye mtima chikungotsalira ndi mwayi” anatero Nkhoma.

Join the conversation — share your thoughts on this story

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.

Discover more from Malawi24

Subscribe now to keep reading and get access to the full archive.

Continue reading