Bokosi, mapemphero ayi! – wasanjiratu mapulani a maliro ake Ray Harawa
Pomwe ambiri sitimafuna kukamba kapena kumva za imfa yathu, mtsogoleri wa gulu loyimba la Black Missionaries, Ray Harawa, waperekeratu zomwe amafuna zidzachitike akadzagona; thupi kuika m’bokosi? Ampingo kupantha uthenga olamitsa? “Za Chiyani?”
Kudzera pa tsamba lake la fesibuku, Harawa waperekeratu zokhumba zake akadzamwalira zomwe zabweretsa mtsutso pa masamba anchezo kaamba koti zina ndizotsutsana ndichikhalidwe komaso chipembedzo cha mbadwa zochuluka m’dziko muno.
Mwazina, iye wati sakufuna maliro ake adzakhale opatsa kaso, kufika paja poti anthu mkumasilira bokosi. Harawa wanenetsa kuti iye pano pomwe ali moyo akukhala m’moyo wa wamba, choncho ndizopanda pake kuti maliro ake adzakhale apamwamba.
“Maliro anga asadzakhale apamwamba chifukwa sindinakhalepo moyo wapamwamba ndipo cholinga changa nthawi zonse nchoti udzakhale mwambo ondiperekeza wophweka. Thupi langa lidzangokulungidwa ndikuyikidwa pa machira, sipadzafunika bokosi,” watelo Harawa muuthenga omwe anaulemba m’chizungu.
Iye walamula kuti pa maliro ake pasadzachitike mwambo ulionse wa chipembedzo monga ulaliki, nyimbo zauzimu, m’malo mwake kudzangokhale kupereka malonje, kukumbukira moyo wake ngati unali ofunika kapena ayi.
Chizolowezi chonyamula maliro kupititsa kumudzi, mwachitsanzo kuwanyamula maliro ku Chitipa kukaika ku Nsanje, Harawa waneneratu kuti zisadzachitike. Iye wati samawona chanzeru chiri chonse kunyamula maliro komwe anali, kuyenda nawo mtunda wautali kuti akaikidwe m’anda.
Harawa wapempha kuti ndalama zomwe ena angafune kudzagwiritsa ntchito kuti mwambo wa maliro ake uwoneke wapamwamba, zidzagwiritsidwe ntchito ina.
“Ndalama zomwe zimayenera kuguliridwa bokosi ndi kwabwino kudzathandizira anthu omwe amadalira ine kapena anthu ena ovutika,” watsindika Harawa. “Ndikusiya zokhumba zanga osati wiro, chifukwa ndilibe chuma chilichonse choti ndingasiyire ena.”
Pakadali pano, mtsutso wakula pa nkhaniyi. Pomwe ena akuyikira kumbuyo Harawa pobweretsa poyera khumbo lakeri, ena akumudzudzula kuti nkhani ngati izi sizimafunika kuzikamba poyera ati kaamba koti nthawi zina zimatha kukubweretsera matsoka.









