Mfumu yagamulidwa zaka 12 pa mlandu ogwiririra ana awiri


Jabu Mailosi Madzi- Malawi24

Bwalo la mirandu la Salima First Grade Magistrate, lagamula mfumu ina kukakhala kundende ndikukagwira ntchito yakalavula gaga zaka 12 chifukwa chogwiririra mabuthu awiri azaka 11 ndi 14 motsatizana.

Malingana ndi wofalitsa nkhani za apolisi ku Salima, Sub Inspector Rabecca Ndiwate, mfumu-yi ndi a Jabu Mailosi Madzi, yomwe ndi Group Village Headman Mzoza.

A Ndiwate ati khothi kudzera kwa woimira boma pa mirandu Inspector Justice Manolo, linamva kuti pa January 1, 2026, mfumuyi inanyengerera atsikanawo, kuwatenga pa njinga yamoto kupita ku Lifidzi Trading Centre komwe inawagulira zakumwa komanso nyama.

Atawadyetsa, Madzi anatenga atsikanawo ndi kupita nawo kutchire lina la m’mudzi wa Ndaluza komwe anawagwiririra motsatizana. Ngati chitseka pakamwa, njondayi inawapatsa mabuthuwa K10,000 aliyense, ndijuwaopseza kuti asauze aliyense za malodzawa.

Koma ataonekera pa bwalo la mirandu, Madzi anakana mirandu yomwe ankayimbidwa, zomwe zinapangitsa boma kuyitanitsa mboni zitatu kufika pomwe adapezeka wolakwa.

Apa woimira boma pa milandu anapempha khothi kuti lipereke chirango chokhwima, ponena kuti monga mfumu ya mudzi, Madzi amayenera kuteteza anthu ake osati kuwachitira nkhanza.

Mbali yaboma inafotokozanso kuti atsikanawo asiyidwa ndi mabala a m’maganizo chifukwa cha zomwe zinawachitikira.

Komabe Madzi anapempha khothi kuti limuchitire chifundo, ponena kuti iye ali ndi udindo wosamalira banja lake.

Apa wogamula mulandu anapereka chilango cha zaka zisanu ndi chimodzi pa mlandu oyamba ndi zina zisanu ndi chimodzi pa mlandu wachiwiri kuti zikhale chenjezo kwa anthu ena.

Zigamulozi ziyenda motsatizana, zomwe zikutanthauza kuti Madzi akakhala ku m’ndende zaka 12.

A Jabu Mailosi amachokera m’mudzi mwa Kabumbu kwa mfumu yayikulu Pemba ku Salima.

Join the conversation — share your thoughts on this story

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.

Discover more from Malawi24

Subscribe now to keep reading and get access to the full archive.

Continue reading