‘Zigamba zili phwee!’ Kapito waseka Mkoka potenga chiletso


Jonh- Malawi24

Mkulu wa bungwe la Consumers Association of Malawi (CAMA), John Kapito wati pano akuwapempherera a Austin Mkoka kuti chiwanda chomwe chawalowa chofuna kuwononga miyoyo ya anthu ambiri chituluke.

A Mkoka, anatenga chiletso ku bwalo la milandu kuti Sipikala wa nyumba yamalamulo, Sameer Suleman kuti asapitirire ndi ganizo lake lokhanzikitsa ma komiti khumi ndi awiri omwe amafuna kufufuza katangale m’boma.

Poyankhula pa msonkhano wa wolemba nkhani, omwe cholinga chake kunali kufotokonza mbali yawo za mmene zotsamwitsa pa nkhani ya mafuta a galimoto komanso magetsi zikukhudzira anthu ogula m’dziko muno, a Kapito anawonetsa kukhumudwa ndi anthu ochepa omwe akufuna kukhutitsa mimba zawo koma a Malawi n’kumavutika.

“Ndani wa mzeru zake angadane ndi kafukufuku wa katangale? Ndiuzeni chomwe Sipikala analakwitsa, munthu zigamba zili phweee nkumakatenga chiletso. Abambo inu ndikukupemphererani kuti mzimu ofuna a Malawi azuzike ukuchokeni” anatero Kapito.

A Kapito anapemphaso a Malawi kuyima limodzi ndi a Sameer Suleman ponena kuti ali pa chiopsezo ndi anthu omwe sakusangala ndi ganizo lokhanzikitsa ma komiti.

Pa nkhani ya ndalama zakunja zomwe zakhala vuto la nthawi yayitali mdziko muno, a Kapito ati pamafunika mtsogoleri yemwe angathetse mchitidwe ogulitsa ndalama zakunja pamsika osavomerezeka.

Iwo anatchula mmene anthu ena andale akukhulira katundu odula, kumanga nyumba zapamwamba, komaso kutsekula ma bizinesi akuluakulu ponena kuti ndi omwe akusangalala ndalama zakunja komaso misonkho ya a Malawi.

“Nthawi yomweyi ena achita kutupa mitu ngati chiweto, ngati alumidwa ndi mavu ineso kumadabwa kuti awa afika kale apa, zonsezo ndalama zakunja komaso misonkho ya a Malawi”

A John Kapito ati pakadali pano apempha oyimira CAMA pa milandu kuti awunikire chiletso chomwe a Austin Mkoka anatenga ku bwalo la milandu ndipo atengapo mbali pofika sabata yamawa.

Kwakhala mpungwepungwe kuchokera pomwe sipikala anakhazikitsa ma komiti khumi ndi awiri ofufuza katangale pomwe chipani cha DPP ndinalemba kalata yotsutsana ndi ganizoli komaso panali kusinthana mau pakati pa a Suleman ndi mneneri wa DPP a Shadric Namalomba.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.

Discover more from Malawi24

Subscribe now to keep reading and get access to the full archive.

Continue reading