Silver Ladies yalonjeza kubweretsa mamendulo


Silver Ladies- Malawi24

Timu ya Silver Strikers Ladies yalonjeza kubweretsa kangachepe pomwe lero ikusewera masewero ake omaliza mu CAF Women’s Champions League COSAFA Qualifiers.

Mphunzitsi wa timuyi Patricio Kulemeka wati Silver Strikers Ladies ibwelera kumudzi kuno itatenga mendulo za Bronze pavute pasavute,ponena kuti awona mofowoka mwawo kuphatikizapo kuchinyitsa zigoli mwansanga.

“Kwambiri anzathu amatichinya mphindi zoyambilira zomwe zawonetsa kuti timu imayamba ndi phuma” anatero Kulemeka.

Mphunzitsiyu wati ali ndichikhulupiliro kuti apata chipambano pa masewera ake omaliza ndi Gaborone United Ladies, ndipo watsindika zobweretsa chipukuta misonzi. “Tikuyenera tipite ndi mendulo ya Bronze kumudzi”.

Iye wati anali ndi khumbo lofuna kukhala akatswiri kapena kukhala achiwiri kwa akatswiri a mu CAF Women’s Champions League koma zavuta.

Pomwe akukumana ndi Gaborone United Ladies lero masana ano, Silver yati idakonzeka kalekale kudzakumana ndi timu ina iliyonse mu mpikisanowu.

Ma timu awiriwa akumana pa bwalo la Gaborone United mdziko la Botswana pomwe akulimbirana okhala pa nambala yachitatu.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.

Discover more from Malawi24

Subscribe now to keep reading and get access to the full archive.

Continue reading