Kukana kuvala chipewa pa kabanza kukuonongetsa chuma chaboma — Ben Phiri


Ben Phiri- Malawi24

Nduna ya zamaboma ang’ono, Ben Phiri yadzudzula anthu omwe amakana kuvala chipewa chodzitetezera akakwezedwa njinga za kabanza, ponena kuti khalidweli likuthandizira kuonongeka kwa chuma cha boma.

Phiri wati boma likuyesetsa kuti ngozi za njinga za moto zichepe koma pali anthu ena omwe salabadira izi ndipo akumasankha kusatsatira malamulo.

Ndunayi yati chokhumudwitsa kwambiri ndichoti ngozi zikachitika boma limawononga ndalama zambiri popereka chithandizo kwa munthu yemwe akanatha kupewa.

“Ndimawona nthawi zina mu mzinda wa Lilongwe, wokwezedwa njinga kukana kuvala chipewa, kaya kumakhala kuyifuna ngozi koma dziwani kuti boma limawononga ndalama yambiri kuthandiza anthuwa kuti achile, ngakhaleso amwalire zimakhala ndalama zawonongeka”

A Phiri anayamika woyendetsa njinga ambiri kuti tsopano akutsatira malamulo ovala chipewa ngati chodzitetezera.

Ndunayi inapemphaso bungwe la Kabaza Association komaso a phungu a nyumba yamalamulo kuti atenge gawo lalikulu polimbikitsa anthu awo kutsatira njira zoyenera zodziteteza pa msewu.

“A phungu tiyeni tigwirane manja kuwonetsetsa kuti anthu athu apewe ngozi za njinga zamoto chifukwa akavulala olo kumwalira amayimbira lamya ife tomwe kufuna thandizo la ndalama”

Ngati njira yolimbikitsira kuvala zipewa, ndunayi yagula zipewa zomwe yagawa kwa woyendetsa njinga zamoto ku dera lawo lapakati m’boma la Thyolo.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.

Discover more from Malawi24

Subscribe now to keep reading and get access to the full archive.

Continue reading