Ndakondwera kuti Scorchers yalephera — JB


Jb- Malawi24

wati Malawi imaika patsogolo zopanda pake

Woyimba Alberto Fernando Zacarias yemwe amadziwika ndi dzina loti Jolly Bro (JB), wati ndiokondwa kuti timu ya Scorchers yalephera pa masewero ake omaliza a WAFCON, pazifukwa zomwe zabweretsa mtsutso.

JB wayankhula izi mukanema yemwe anapanga wa pompopompo potsatira kugonja kwa timu ya atsikana ododa chikopa, Scorchers 0:3 ndi timu ya Cameroon Lamulungu pa masewero omaliza a mpikisano wa WAFCON.

Zacarias, yemwe akukhala mdziko la America, wati kunali kovuta kuti timu ya Scorchers ichite bwino pa masewerowa ponena kuti pali zinthu zambiri zomwe dziko lino limamukwiyitsa nazo Mulungu.

Apa JB anapereka chitsanzo choti dziko lino linayika chidwi chochuluka ku mpirawu chonsecho pali anthu ochuluka omwe akuvutika ndipo akufuna thandizo la ndalama ngati zomwe Scorchers yagwiritsa ntchito ku mpikisanowu.

“Mumaona ngati mupita nazo kuti, Mulungu sangakondwere ndi dziko loyika patsogolo zinthu zopusa. Mpira zoona? Kodi ife timadya mpira?

“Mukoze kaye misewu, magetsi, madzi komaso muthetse umphawi. Tawathandizani kaye anthu osauka zinazo pambuyo. Pali zinthu zambiri zomwe tingaziike patsogolo osati mpira, mpira wakeso wa azimayi zoona?” Watero JB.

Iye anapitiriza kuyankhula ndikudabwa kuti a ndale ambiri anakwera ndege kuyitsata Scorchers pa masewero ake omaliza chonsecho ndalama zakunja zikusowa m’dziko muno.

JB wati kukanakhala bwino a ndale atabwera pamodzi kupanga chitukuko, ngati mmene anachitira posapota timu ya Scorchers.

Mkuluyu anamaliza ndikuchenjeza kuti anthu mdziko muno apitirirabe kuchakachika ndi umphawi ngati chidwi cha a tsogoleri chipitirire kukhala pazinthu zomwe wati ndiza msangulutso chabe.

Zomwe wayankhula JB zabweretsa mtsutso pakati pa anthu omwe anathamangira ku tsamba la woyimba Hip-Hop’yu.

Gulu lina la anthu lati likugwirizana ndi JB ponena kuti mpira ukuyenera kukhala chinthu chomaliza pa zinthu zofunika monga misewu, zipatala ndi sukulu.

“Ndipo sukunama ase, pena pake ndife anthu ogona kwambiri, imagine ndalama zagwira ntchito zi zikanapita ku health sector?” adatero wina mogwirizana ndi JB.

Komabe, gulu lina la anthu lamutsutsaso JB ponena kuti masewero nawoso pawokha ndi chitukuko ndipo ali ndikuthekera kobweretsa ndalama mdziko.

“Tapeza forex $1.5 million through scorchers” mmodzi mwa anthuwa anatero.

Wina anadabwa ndimaganizidwe a JB ponena kuti mpira ndichimodzi mwa zinthu zomwe zikuthandiza kulemba ntchito achinyamata pomwe wina anawuza JB kuti anthu omwe anapita ku Morocco anagwiritsa ntchito ndalama za mthumba mwawo.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.

Discover more from Malawi24

Subscribe now to keep reading and get access to the full archive.

Continue reading