Zonyera Zambuzi alongedwa kukhala Senior Chief Kachindamoto VIII


Mwambo Omveka Mkanjo A Zonyera Zambuzi- Malawi24

A Enoch Zonyera Zambuzi Kalapino azaka 61, awalonga ufumu kukhala Senior Chief Kachindamoto VIII, ndipo alowa m’malo mwa malemu Senior Chief Theresa Chidyaonga Kachindamoto VII, m’boma la Dedza.

Mwambowu unachitikira pa bwalo la zamasewero la Dedza, m’bomali ndipo ufumu wa Kachindamoto wakhala opanda munthu kuchokera chaka chatha pomwe malemuwa adalowa m’manda.

A Zonyera Zambuzi awalonga ufumu kutsatira pomwe Inkosi Ya Makosi Gomani V, inavomereza dzina la a Zonyera Zambuzi kukhala mlowam’malo wa ufumu wa Kachindamoto.

Poyankhulapo pamwambowu, Nduna yoona zamaboma ang’ono, a Ben Malunga Phiri, alangiza Mafumu andodo m’bomali, kuti apewe kuyitanitsa ndalama kwa mafumu ang’onoang’ono omwe akufuna kuwakweza ufumu, zomwe anati ndizopereka chitsanzo choipa.

Zonyera Zambuzi Kalapino- Malawi24
Zambuzi

A Phiri amayankhula izi pomwe amalangiza a Zonyera Zambuzi munthawi yomwe amawaveka mkanjo kukhala Senior Chief Kachindamoto VIII.

A Phiri anati a Zonyera Zambuzi atengere chitsanzo chabwino cha malemu Senior Chief Theresa Kachindamoto Vll.

Malinga ndi a Phiri, malemu Senior Chief Theresa Kachindamoto anakwanitsa kuthetsa maukwati a ana okwana 3,500 ndikuwonetsetsanso kuti ana akupita ku sukulu.

Apa mfumu yomwe inayimira Ngwenyama iNkosi Ya Makosi Gomani V, Senior Chief iNkosi Makwangwala alangiza mafumuwa kuti asamalande malo kwa anthu.

Mfumuyi inapitilira ndikumema anthu kuti azilemekeza mafumu awo.

Kupatula kulonga ufumu a Zonyera Zambuzi kukhala mlowam’malo wa ufumu wa Kachindamoto, mafumu enanso awakweza kukhala ma gulupu pamwambowu.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.

Discover more from Malawi24

Subscribe now to keep reading and get access to the full archive.

Continue reading