Njonda ina yomwe imapapira mowa ku LeyLand Bar ku Bwandilo munzinda wa Lilongwe yaombera munthu pokwiya ndikukumbutsidwa ngongole ya mowawo.
Malinga ndi m’neneri wa polisi ya Lingadzi ku Lilongwe Maria Kumwenda, mkuluyu yemwe ndi Romario Lolenzo, 31, anakwiya atafunsidwa ndi mwini malo omwerawa, Fauzia Issa kuti alipire ngongole yamowa yokwana k116,000.
Pokwiya ndikufusidwaku, Lolenzo anayamba kuchita zachiwawa mpaka kutulutsa mfuti ya mtundu wa pistol ndi kuwombera mlengalenga, kenako ndikudzawomberanso pansi.
Pofuna kumulanda mfutiyo, Yazeed Mussa Hamdan, anakankhira Lolenzo pansi, kenaka Lolenzo anawombera kawiri m’matako Zakir Mussa Hamdan yemwe ndi mchimwene wa Yazeed.

Zakir anatengeredwa polisi ya Lingadzi asanamutumize ku chipatala chachikulu cha Kamuzu Central kuti akalandire chithandizo.
Malingana ndi a Kumwenda, Zakir ali bwino ndipo akulandira chithandizo kuchipatala.
Kumwenda wati Lolenzo wanjatwa pa mlandu wogwiritsa ntchito mfuti mosaloledwa komanso kuchita zinthu pofuna kuvulaza munthu, pomwe kafukufuku wa polisi ali mkati kuti adziwe ngati mfutiyo ndiyolembetsedwa mwamalamulo.
