A Ken Msonda omwe ndi wachiwiri kwa mneneri wa chipani chotsutsa boma cha Malawi Congress (MCP) wadzudzula anthu ponena kuti “adatukwa munthu osalakwa” a Lazarus Chakwera pa ngozi ya ndege, ndipo wati kafukufuku wa ngoziyi athe asapitirire.
Poyankhula mu kilipi ina (audio clip) yomwe anthu akugawana m’masamba amchezo, Msonda wati potengera momwe kafukufuku wangoziyi wayendera masiku amenewa, sipakufunikaso kuti apitirire ponena kuti chilungamo chadziwika kale.
“Chimene a Malawi ambiri amayembekezera kuti chitha kusintha panopa zadziwika kuti palibe chomwe chisinthe. Amaliza nkhani ija ndi akubanja kwa malemu Ralph Kasambara, akuluakulu aku foreign affairs, makamakaso akuluakulu aku Malawi Defense Force, a General George Jafu ndi General Dr Paul Valantino Phiri,” watero Msonda.
Iye wati anthuwa apereka umboni ogwirika ndipo sikofunikaso kuti kafukufuku pankhaniyi apitirire ponena kuti kutero kungokhala kuwononga ndalama za misonkho.
“Ine maganizo anga ndikuti commission of Inquiry ija itithera ndalama zathu za misonkho, bola ingotha,” watero Msonda.
Iye wati ndizodandaulitsa kuti anthu adathera zakukhosi mtsogoleri wa kale wa dziko lino a Chakwera pangoziyi omwe wati kwa iye ndiosalakwa.
“Ndizovetsa chisoni kuti tinanyoza, tinatukwa tinalalatira munthu osalakwa pulezidenti wathu wakale Dr Lazarus Chakwera chifukwa chofuna mipando pa ndale,” wateroso Msonda. “Achakwera adalira, moyo wawo unali osweka. Mulungu pano yakwana nthawi kuti nawoso a Chakwera asekelele muntima.”
Potsiriza, Msonda wati ndi kwabwino kuti ndalama zomwe zikukugwira ntchito pa kafukufukuyu zigwiritsidwe ntchito zina zomwe zikhale zopindulira anthu m’dziko muno.
“Ine ndikuti ndalama za misonkho tipulumutse, mwina tithandizire anzathu akuchokera ku South Africa’wa akawone poyambira, mwina tithandizeso kuti petrol, fetereza ndizina zitsike. Tikapanda kutero titha chaka anthu aja akulandira ma alawasi pamene nkhaniyi yatha kale,” watsindika Msonda.
Komiti yapadera ya ku nyumba ya malamulo yomwe ikufufuza tsatanetsatane wa ngozi yomwe idapha a Saulos Chilima ndi ena 8 pa 10 June, 2024, ikutolera umboni kuchokera kwa anthu okhudzidwa osiyanasiyana.









