Apolisi m’dziko la India apulumutsa abambo khumi ndi awiri (12), omwe amasungidwa mu fakitole ina ndikumagwira ntchito mwakalavula gaga.
Abambowa adalonjezedwa ntchito ya mu fakitole koma chosadziwa zinthu zidayamba kusintha pamene adalandidwa ma foni awo ndipo panalibe kulumikizana ndi abale kwa miyezi.
Iwo ati amakanizidwa kusiya ntchitoyo komanso amagwira ntchito osapumila ndipo akapempha malipiro amamenyedwa kodetsa nkhawa.
Nkhaniyi idadziwika apolisi atatsinidwa khutu ndi anthu ena kuti ku fakitoleyi kuli ogwira ntchito omwe amasungidwa ngati akayidi.
Anthuwa ati akamadya chakudya pamakhala pali agalu olusa omwe amalondera anthuwa ndipo amadya kamodzi pa tsiku.
Akatswiri oona za maufulu a anthu m’dzikolo adzudzula mchitidwewu ndipo ati izi zifufuzidwe bwino ndipo onse okhudzidwa alindire chilango malinga ndi malamulo.
Source: BBC
Apolisi mdzikolo adakafufuzabe za nkhaniyi kaamba koti pali malipoti oti ogwira ntchito ena adafera mu fakitoleyi kamba kakuchitiridwa nkhanza.
Pakadali pano apolisi amanga anthu awiri omwe akuwaganizira kuti akukhudzidwa ndi nkhaniyi koma mwini fakitoleyi wathawa ndipo sakudziwika komwe ali.









