Akabaza akudyeredwa masuku pamutu


Kabaza- Malawi24

Ndalama yomwe ochita kabaza amayenera kudya ndi maanja awo, inde kudzipepesa atawombedwa ndi mphepo pansewu, ikuthera m’matumba mwa adindo omwe akumawanamiza kuti awathandiza kupeza ngongole ya boma.

Kafukufuku wa Malawi24 wapeza kuti akuluakulu a Kabaza Association of Malawi (KAM) akutolera ndalama kwa anthu ochita kabaza mdziko muno powauza kuti akatero awalemba kuti apindule nawo pangongole za boma.

Kwa miyezi ingapo takhala tikuyankhulana ndi adindo oyang’anira anthu ochita kabaza m’madera ena ku Nkhotakota, Monkebay komaso madera angapo mu mzinda wa Lilongwe omwe akhala akupereka madandaulo ofanana.

Ambiri mwaiwo ati kuyambira 2019 mpaka pano, akuluakulu a KAM akhala akuwauza kuti wakabaza aliyese m’madera awo alipire ndalama za khadi la RTN, yaziphaso zoyendera pa mseu, yolembetsera njinga komaso ngongole, zomwe ati sizikumaoneka komwe zikumapita.

“Chodabwitsa ndichoti kuno ku Monkeybay anachita kulumikizana ndi apolisi apa mseu achigawo chakummawa kwa dziko lino ndipo chitengere ndalama yathu sitiwonaso tsogolo,” anatero m’modzi mwa adindowa yemwe anapempha kuti tisamutchule.

Sabata ino, nthumwi za KAM, zinaliso mu mzinda wa Blantyre komwe zimakumana ndi adindo akabaza kuchokera mumzindawu komaso maboma ena ngati Phalombe, Zomba ndi Mulanje, komweso ayitanitsa ndalama monga momwe akhala akuchitira m’madera ena.

Andrew Mwendanato Njinga Association- Malawi24
Mwendanato: Nafeso talandirapo madandaulo ngati awa

Kafukufuku wathuyu wapeza kuti anthuwa akumagwiritsa ntchito a polisi, maka a nthambi ya Victim Support Unit omwe akumayimbira lamya apampando akabaza m’mabomawo kuti achite mkumano.

Apampandowa akumauzidwa njira zotolera ndalama kwa anthu awo zomwe ndizoposera K100,000 aliyese, ndipo akumauzidwa kuti kulembetsa njinga komaso ngongole zimadzera ku banki ya NBS.

Titafusa m’modzi mwa wogwira ntchito ku NBS, a Chiyamiko Lita anatiyankha kuti NBS sikukhudzidwa nawo ndipo amenewo ndi akuba chabe.

Anthu ochita kabazawa akhalaso akufusa mafuso kuti anthu omwe siwolembedwa ndi boma, koma akumagwira njinga zamoto ndikumalipitsa oyendetsa, amatumidwa ndi ndani?

Mu tawuni ya Lilongwe, muli anyamata ovala ma rifurekitara ndipo amagwiritsa ntchito njinga ya apolisi kumagwira akabaza ndikumawalipitsa ndalama zomwe sizidziwika komwe zimapita.

Takhala tikuyesa kuyankhula ndi unduna wazachitetezo chamdziko komaso nthambi ya polisi yoyang’anira zapamsewu kuti ayikepo mlomo pa nkhanizi koma zakhala zikukanika.

A Andrew Mwendanato omwe ndi mkulu wa Njinga Association yomweso imayang’anira za njinga zakapalasa komaso zamoto, anati nawoso akhala akulandira madandaulo kuchoka kwa akabaza omwe akhala akuberedwa mu njira zomwezi.

A Mwendanato ati kumbali yawo ngati bungwe, akhala akuyankhula ndi unduna wazachitetezo cha mdziko kuti uchitepo kanthu pamadando omwe anthuwa akumapereka.

Chachidziwikire ndichoti ngati adindo sachitapo kanthu msanga, anthu ochita kabaza apitilira kudyeredwa masuku pamutu. Koma fuso mkumati, adindo oyenera kuchita kanthuwo achokera kuti popeza oyenera kuterowo ena mwa iwo akukhudzidwa ndi nkhaniyi pomwe adindo ena sakuonetsa chidwi.

Wakabaza apange bwanji? Ndalama yomwe amaipeza atakhetsa thukuta, kuombedwa ndi mphepo, itha kupitirira kuthera m’matumba mwa anthu olakwika.

Join the conversation — share your thoughts on this story

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.

Discover more from Malawi24

Subscribe now to keep reading and get access to the full archive.

Continue reading