Kutakhala kupsa ndekuti kukhala kwa chigumu, pamwamba moto, pansi moto:; pena nkumafusa kuti kodi mayikowa achita kugwirizana kuti a Malawi tiwakhaulitse asamatuluke kunja?
Posachedwapa, dziko la America lalengeza kuti lichotsa ofesi zopangira zilolezo zopitira mdzikolo m’mayiko ena kuphatikizapo Malawi zomwe zichititse kuti a Malawi ochuluka adzilephera kupitako.
Pa mwamba pa zonsezi, ku South Africa ndi uku kwakhwithimaku. Anthu kuphatikizapo a Malawi akuzunzidwa pomwe nzika za dzikolo zati sizikufuna alendo adziwatengera ntchito zomwe iwo amayenera kumagwira.
Khalekhale, nalo dziko la Kuwait laika Malawi kukhala limodzi mwamaiko amu Africa oletsedwa kutumiza anthu okagwira ntchito zammakomo (Domestic Workers).
Kuwait yatulutsa kalata yosonyeza mndandanda wa maiko 27 omwe sakuyenera kumatumiza anthu m’dzikolo.
Kupatula Malawi, ena mwa mayiko omwe akhudzidwa ndi Nigeria, Kenya ndi Angola ndipo maiko omwe aloledwa ndi monga South Africa, Ethiopia ndi Benin,pomwe la Senegal lauzidwa kuti anthu omwe angawalole kukagwira ntchito ndi amuna okha basi.
Dzikoli silinafotokoze bwino zifukwa zomwe lapangira ganizoli.
Zatelemu zikutanthauza kuti a Malawi ambiri omwe amapita ku Kuwait, South Africa komaso America kukagwira ntchito, asowa kolowera.
Pakadali pano, boma la Malawi silinayankhulepo pa ganizoli.