Boma liyamba kumanga msika wapamwamba m’tawuni ya Lilongwe mwezi uno


Ben Phiri Minister Of Local Government- Malawi24

Pali chiyembekezo kuti tawuni ya nzinda wa Lilongwe ivala maonekedwe atsopano komaso ntchito za malonda zifikira mlingo wina pomwe boma lati mwezi uno usanathe liyamba kumanga msika wa nyumba zosanjikana.

Izi ndi malingana ndi nduna ya zamaboma ang’ono, Ben Phiri yemwe amayankhu lero Lamulungu pa bwalo lazamasewero la UNICEF kwa Chinsapo, mu mzinda wa Lilongwe pomwe amachititsa msonkhano omema anthu kuti adzasankhe a Mike Chimzukira ngati phungu wa delari pa chisankho cha chibwereza chomwe chidzachitike pa 30 June.

“Pasanafike pa 30, tiyamba kumanga msika wamakono wa nyumba zosanjikana mu tawuni ya Lilongwe. Tikatero ndiye kuti chitukuko chayamba kale kumutsata Mike chifukwa izi zchiitika mu dera lomwe lino,” watelo Phiri.

Kupatula msikawu, ndunayi yawululaso kuti ku derali kuyambitsidwa mpikisano wa masewero a mpira wa anyamata komaso atsikana, komaso mpikisano wa m kwaya kuti achinyamata asamasowe zochita.

A Phiri anawuzaso anthu a derali kuti asankhe a Chimzukira chifukwa akuyimira chipani cholamula cha Democratic Progressive Party (DPP), kotero kudzakhala kosavuta kupempha chitukuko ku boma.

“Kukhala njala kunjaku, kufunika ngongole kuno kukhala zofunika zambiri ndipo munthu wake opempha ndi Mike,” anatero a Phiri omweso anauzaso anthuwa kuti K500 miliyoni yachitukuko cha mmadera, ikufunikiraso anthu a mzeru ngati Chimzukira.

Pa msonkhanowu panaliso nduna yowona kuti pasamakhale kusiyana pakati pa amuna ndi akazi, anthu awulumali komaso chisamaliro cha okalamba, Mary Navicha omwe anawuza anthuwa kuti adzasankhe a Chimzukira ngati phungu wawo potengera kuti chitukuko kumadera chimafika ndi a Phungu a DPP.

A Navicha anayamikira mtsogoleri wa dziko lino Peter Mutharika powonetsetsa kut chakudya chikupezeka paliponse chotsika mtengo komaso kuthetsa malipiro amaphunziro ku sukulu za sekondare zomwe ati zachepetsa chipsinjo kwa a Malawi.

Bungwe loyendetsa chisankho la MEC linalamula kuti anthu asankheso phungu wa Lilongwe Bwaila, kutsatira kuyimitsidwa kwa zotsatira zomwe anthu ena anakadandaula kuti zinali ndi zotsamwitsa zambiri.

Join the conversation — share your thoughts on this story

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.

Discover more from Malawi24

Subscribe now to keep reading and get access to the full archive.

Continue reading