Mighty Wanderers yagwaza Karonga United


Fdh Premiership- Malawi24

Pomwe kamtoletole wa ma points mu mpikisano wa FDH Bank Premiership walowa sabata ya chisanu ndi chimodzi, timu ya Mighty Wanderers yaumbudza timu ya Karonga United 4-1, pomwe tsopano yabwera pa nambala yachitatu.

Masewerowa omwe amkayenera kukhala otsekulira FDH Bank Premiership koma adalephereka kaamba kakusamvana pakati pa SULOM ndi FAM pa nkhani ya bwalo la Kamuzu, analipo Lachitatu pa bwalo la Mpira ku Chiwembe mu mzinda wa Blantyre.

Anayambitsa zonse adali chiyambakale Isaac “Chair” Kaliyati yemwe ndi mwendo wake wa manzere anamwetsa chigoli pa mphindi ya 15. Patangotha mphindi 7, Lameck Mithi yemwe Manoma agula posachedwapa, anasumbira muukonde kona yomwe Kaliyati anasema.

Wanderers- Malawi24
Wanderers kumwemwetera.

Mithi anagwedezaso ukonde pa mphindi ya 38 komaso 88 zomwe zinapangitsa kuti asankhidwe kukhala wosewera yemwe anasewera bwino pa tsikuli.

Kupatula zigolizi, anyamata a ku Lali Lubani’wa anagogoda kangapo konse pa golo la Jamu, koma mabomba awo amangothera kuwomba zitsulo za golo.

Karonga inakanilatu kubwerela kwawo chimanjamanja. Alex Benson anamwetsa chigoli cha chipukuta misonzi pomwe anyamata otchinga kumbuyo kwa Wanderers anagwidwa njengunje, ndipo anangomenya ka mtosi kumudutsa Dalitso Khungwa.

Polankhula atatha masewerowa, mphunzitsi wa Wanderers Bob Mpinganjira anati timu yake inali ndi kuthekera kogoletsa zigoli zambiri koma zangovuta. Iye wati ndiokhutitsidwa ndi ma points khumi omwe Noma yapeza pa masewero asanu.

Mphunzitsi wa Karonga United Audro Makonyola anati osewera ake analibe mantha ndi Wanderers koma kungoti ena ndi achichepere kwambiri.

Iye anati anakakamizika kugwiritsa ntchito anyamata ena omwe ndi ovulala kuchokera m’masewero omwe apita.

Makonyola wati Karonga ipitilira kusula osewera, omwe ena mwa iwo omwe asula kale akuthandiza ma timu amene akuchita bwino pakadali pano.

Zatelemu Wanderers ili pa nambala yachitatu tsopano pa m’ndandanda ndi ma point ake 10 chimodzimodzi Silver Strikers pomwe akungolekana chigoli chimodzi pamene Karonga United iri pa nambala 12 ndi ma point 5 onse mu maseweronso asanu.

Join the conversation — share your thoughts on this story

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.

Discover more from Malawi24

Subscribe now to keep reading and get access to the full archive.

Continue reading