Mkumano wa makhansala ku Zomba walephereka chifukwa chachisokonezo

Advertisement

Mkumano wa nambala 19 wama Khansala komanso wa Phungu yekhayo wamu mzinda wa Zomba omwe pachingerezi umatchedwa Full Council walephereka chifukwa chachisokonedzo chomwe chidabuka munyumbayi.

Makhansala achipani cha DPP komanso Phungu wachipani cha DPP Bester Awali adafunsa Mfumu ya Mzinda wa Zomba Khansala Davie Maunde kuti ndichifikwa chiyani adalepheretsa mkumano womwe umayenera kuchitika Lachisanu pa 2 February.

Poyankhulapo, Mfumu ya Mzinda wa Zomba Khansala Davie Maunde adakumbutsa nyumbayi kuti zomwe akunena makhansalawo ndizotsamveka chifukwa nkhaniyi adayikambirana kale pa gulupu yawo lapa Whatsapp lomwe makhansala ochuluka adamvomereza kuti mkumanowo uchitike Lolemba pa 5 February.

Ndipo chifukwa chakusamvana komanso kulodzana dzala komwe kudabuka pakati pawo, Mfumuyi idalamula kuti mkumanowo ulephereke mpaka mtsogolo muno.

Pamenepa Khansala Davie Maunde wadzudzula makhansala komanso phunguyu chifukwa choyambitsa chisokonezo zomwe zapangitsa kuti zokambiranazi zilephereke.

Advertisement