Chipani cha Malawi Congress (MCP) chatsindika kuti sichitenga nthawi yayitali chiri mbali yotsutsa boma ponena kuti chibwereranso m’boma mu 2030.
Phungu wa nyumba ya malamulo wadera la mchingawo chapakati ku Kasungu, Chikondi Kampachike Chisale, ndiye wanena izi pamene amapempha ndikulimbikitsa otsatira chipanichi kuti asataye mtima.
Iye wati kusachita bwino kwa chipanichi pa chisankho cha 2025, kusawafooketse koma kuwalimbikitse kuti akonzenso zinthu zina kuchipanichi ndikukhalanso chipani cha mphamvu.
Poyankhula pa mkumanowu, phunguyu anati chipani cha MCP ndi chamoyo ndipo chiri ndikuthekera kobwereranso m’boma ngati mamembala ake agwiritsa ntchito zaka zikubwerazi pokonzanso ngodya za chipanichi mdziko muno.
Iye anati munthawi yomwe dziko lino likulowera mchaka cha masankho cha 2030, chipanichi chigwiritse ntchito nthawiyi pounika mwa zina zomwe zidapangitsa kuti chipanichi chisachite bwino pa chisankho cha chaka chatha, ndikukonza pomwe pakufunika kukonza kuti chipanichi chithe kuika chikhulupiliro kwa anthu ovota.
Kampachike Chisale wapemphanso otsatira chipanichi kuti akhale ndi umodzi pamene chipanichi chikuyembekezera kusankha adindo atsopano mchipanichi pa mipando yosiyanasiyana. Iye anati mgwirizano wamkati mwa chipanichi uthandiza kuti chipanichi chidzakwanitse kulamuliranso.
Mkumanowu ukudza pomwe chipani cha MCP chikuyamba zokonzekera chisankho chofuna kuika adindo osiyanasiyana mipando mchipanichi.
Wapampando wadera la chigawo chapakati Yolamu Chimbalani, wayamikira Kampachike Chisale pochititsa mkumanowu, ponena kuti wabwera munthawi yake yoyenera kutsatira kugonjetsedwa kwa chipanichi pa chisankho.
Chimbani anati mkumano walimbikitsa ndikupereka mphamvu kwa otsatira chipanichi komanso kukolezera kudzipereka kwawo ndicholinga chofuna kuti akwaniritse cholinga cha MCP chobwereranso m’boma mu 2030.
Chipani cha MCP chidachotsedwa m’boma pa chisankho cha pa 16 September, 2025, pomwe mtsogoleri wa chipanichi Lazarus Chakwera adagonjetsedwa ndi mtsogoleri wa chipani cha DPP Peter Mutharika yemwe akulamula pano.









