Pomwe ligi yaikulu ya FDH Premiership ikubwerera m’bwalo lero, matimu achenjezedwa ofuna pagolo pa Ekhaya avale dzilimbe apo bii sapaona.
Mphunzitsi wa Ekhaya Fundi Akidu, wati limodzi mwa vuto lomwe timuyi yakumana nalo mchigawo choyamba chapitachi, ndilogoletsetsa zigoli zochuluka.
Akidu amalunkhula izi Lachisanu pomwe Ekhaya ikuyembekezeka kuzepulana ndi Kamuzu Barracks lero Loweluka pa bwalo la Mpira ku Chiwembe mu mzinda wa Blantyre.
Mphunzitsiyu wati vuto lochinyitsa ndilomwe lathandizira kuti timuyi isachite bwino mchigawo choyamba cha ligiyi.
“Ndife akatswiri a Airtel Top8 inde koma mu mpikisano wa FDH Premiership sitinachite bwino, tachichinyitsa zigoli pa masewero aliwonse,” watelo Akidu.
Komabe, iye wati ena mwa mavuto omwe analipo akonzedwa tsopano, ndipo akuyembekezeka kuti timuyi ichita bwino mchigawo chino cha kamuthemuthe, ndipo wati khumbo lawo ndilochinyitsa zigoli zochepa.
Apa, Akidu wamema osewera a timuyi kuti alumire mano mchigawo chimenechi.
Chigawo chachiwiri cha FDH Bank Premiership chikuyambiranso lero ndi masewero anayi, ndipo Ekhaya ikuyamba masewero a mgawo lachiwiri iri pa nambala 11 ndi ma point ake 18.
Timuyi iyamba chigawo chachiwirichi ilibe mphangala yake ina Chimwemwe Chunga yemwe ali ndi zikalata zachikasu zingapo.
Kamuzu Barracks yomwe pakutha pa gawo loyamba inali italandira zikalata zachikasu 21 ndi zofiira zitatu, ikuyamba mgawo lachiwiri iri kumusi pa nambala 15 ndi ma point ake 12.

