Boma lati a Malawi akuyenera kumayamika kuti pano mitengo ya katundu m’dziko muno ikukwera monverera poyelekeza ndi nthawi ya ulamuliro wa Malawi Congress Party.
Izi ndi malingana ndi nduna ya zofalitsa nkhani Shadric Namalomba yemwe Lachisanu amalunkhula ndi imodzi mwa nyumba zowulutsa nkhani m’dziko muno.
Namalomba wati mavuto ena amene analipo muulamuliro wa MCP amakhala mbiri ya make dzana kuchokera pomwe a Malawi anasankha a Peter Mutharika kukhala m’tsogoleri wa dziko lino.
Mwa zinthu zina, iwo ati nthawi ya boma lapitali a Malawi ambiri amasowa chakudya ndipo amagula chigoba cha chimanga pa mtengo wa k15, 000 zomwe zimapangitsa kuti ena azigona ndi njala ngakhale kufa kumene.
“Chimanga chinali chodula, a Malawi ambili amasowa chakudya, kusowa ndalama kuti mpakana ena kumagona ndi njala, ena kumafa kumene,” adatero a Namalomba.
Ndipo mukuyankhula kwawo a Namalomba ati izi ndi zina mwazifukwa zimene a Malawi ambili anaganiza zochotsa boma la Malawi Congress Party ndikusankha boma la Democratic Progressive Party (DPP) ndi Peter Mutharika kuti atsogolele.
Iwo adatinso nthawi imeneija a Malawi ambili analibe maufulu ndipo yense ofuna kuyankhula zosiyana ndi boma amatha kuvulazidwa ngakhale kuwonongetsa katundu.
“Ukangoti uyankhule pang’ono kapena kuti bomali mwalakwitsa mukanapanga chonchi, basi nthawi yomweyo kukutumizilani anyamata a zikwanje kukukhapani khapani katundu wanu kukuwotcherani wotcherani”. Iwo adatero.
Mukuwona kwawo, a Namalomba ati pano palibe wina aliyense amene wazunzika chifukwa chakuti anthu ali ndi ufulu.

