Gwamba walapaso


Gwamba- Malawi24

“Moti nthawi yoseyi mumatsitsimula miyoyo kwinaku mukukonkha?” Achuluka mafuso pa zomwe woyimba nyimbo zauzimu koma zogwira palisani, Duncan Zgambo, wotchedwaso kuti Gwamba wanena.

Woyimba Gwamba waulura kuti wakhala akukokera anthu ku ufumu wa Mulungu kwinaku akukonkha chakumwa chaukali.

Izi ndi malingana ndi zomwe “Landlord” walemba patsamba lake la fesibuku. Lolemba madzulo, Zgambo yemweso amadzitchaso kuti G.O.A.T adadzidzimutsa gulu pomwe adalengeza kuti wasiya kumwa bibida.

“I WILL NEVER DRINK ALCOHOL AGAIN. (Sindidzamwaso mowa),” watelo Gwamba polapa.

Paja mbuto ya kalululu idakula ndi tadzaonani, m’kuthwanima kwa diso anthu adaitanizana ndipo ndemanga zidafumbula pa tsambali.

Ambiri mwa anthu omwe ayikira ndemanga pa tsambali awonetsa kudabwa ndi zomwe woyimbayu walembazi.

“So you’ve been gospeling while drinking holy water😅 (Moti wakhala ukuimba zauzimu ndikumamwaso mowa?),” uno kunali kudabwatu kwa Kelvin Mnkhumbwe, m’modzi mwa oyikira ndemanga.

Naye Happy Kamanga wati wakhala akuganiza kuti Gwamba adasiya kumwa mowa kuyambira pomwe adalengeza kuti wabadwa mwatsopano, wayamba kuimba nyimbo zauzimu. “Thought you stopped a long time ago? 😅😅”

Ena mwa anthu omwe ayikira ndemanga ati woyimbayu akungoserewula chabe ponena kuti munthu wofuna kusiya kumwa mowa samachita kulengeza.

Izi zikubwera pomwe mu 2021, Gwamba adalengezaso kuti wasiya kumwa mowa komaso mankhwala ozunguza ubongo.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.

Discover more from Malawi24

Subscribe now to keep reading and get access to the full archive.

Continue reading