Ophunzira ku Kasungu alonjezedwa thandizo


Chithunzi Chagulu- Malawi24

Ophunzira omwe asankhidwira m’sukulu za sekondale za boma ku Kasungu, alonjezedwa kuti palibe asiyire sukulu panjira kaamba kosowa ndalama za fizi.

Izi ndi malingana ndi phungu wa dera lapakati m’boma la Kasungu, Chikondi Kampachike Chisale yemwe wati awonetsetsa kuti ophunzira ochepekedwa adzithandizidwa kudzera mu thumba la ndalama zakudera (CDF) kuti asalephere maphunziro awo kaamba ka umphawi.

A Chisale amayankhula izi Lachitatu pa sukulu ya pulayimale ya Suza m’bomali pamwambo otsanzikana ndi ophunzira omwe asankhidwa kupita ku sukulu za sekondale za Kasungu komanso Chayamba.

Malingana ndi phunguyu, maphunziro ndilo gwero la chitukuko, choncho ophunzira aliyese sayenera kulephera kupitiriza maphunziro chifukwa cha mavuto azachuma.

Pofuna kulimbikitsa ophunzira omwe asankhidwa kupita ku sukulu zogonera komko, phunguyu wapereka mphatso yazikwama zonyamulira katundu kwa ophunzira asanu.

M’modzi mwa ophunzira emwe walandira nawo mphatsoyi, Lontia Mwanyongo wayamikira phunguyu ponena kuti thandizoli labwera munthawi yake, ndipo wati pa iye yekha sakanakwanitsa kupeza chikwamachi.

A Lyness Mwale omwe ndi kholo la mwana yemwe amusankhira ku sukulu ya Chayamba anati nkhani ya basale ayilandira ndichimwemwe ponena kuti izi zithandiza pomwe iwo alibe mtengo ogwira.

Naye mphunzitsi wamkulu pa sukuluyi, a Thokozani Feliad Chimpiko wati ndi osangalala kaamba kathandizo lomwe phunguyu wapereka.

A Chimpiko ayamikiranso ophunzirawa kaamba kochilimika pa maphunziro awo pomwe sukuluyi yakhonzetsa ana 38 mwa ophunzira 41 omwe adalemba mayeso.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.

Discover more from Malawi24

Subscribe now to keep reading and get access to the full archive.

Continue reading