Zadziwika kuti abambo ambiri ku Malawi kuno omwe anakayezetsapo DNA kuti adziwe ngati ana omwe ali nawo m’banja mwawo alidi awo, ambiri anabwerako atakhumudwa.
Katswiri wa sayansi ya majini, Kingdom Kwapata, wauza nyuzipepala ya The Nation kuti zotsatira za mayeso a DNA omwe wapangapo, zikuonetsa kuti abambo ambiri adapakidwa ana omwe si awo.
Kwapata wati mwezi ulionse amayeza DNA anthu 30, kutanthauza kuti katswiriyu amayeza anthu opitilira 400 pa chaka. Iye wati pa abambo omwe adapita kukayezetsa DNA, 80% adapezeka kuti ana omwe adauzidwa kuti anali awo, adangopakidwa sanali awo enieni.
“Pafupifupi 80% ya mayeso a DNA omwe amuna amachitidwa chifukwa cha kukayikira, 80% amatsimikizira kuti kukayikira kwa amunawo kunali kolondola,” Kwapata wawuza The Nation.
Nayo Attestation Background Checks and DNA Limited Malawi, yomwe ili ndi zipatala ku Blantyre ndi Lilongwe, yakambaso za chiwerengero cha 80% cha ana omwe amapezeka kuti bambo awo si omwe akuwadziwawo akapita kukayezetsa DNA
Ibrahim Swed, wabizinesi ku Lilongwe, ndi m’modzi mwa amuna omwe anapita kukayezetsa DNA chifukwa cha kukayikira komwe anali nako kwa nthawi yayitali. Anayezetsa mu 2022 ndipo zotsatira zina zinatsimikizira kuti ana ena sanali ake.
“Pano sindikhulupiriraso akazi. Pa ana onse amene ndinauzidwa kuti anali anga, ndinakayezetsa DNA kuti nditsimikizire,” watelo Swed.
Nkhani ngati izi zikukolezera kwambiri kutha kwa mabanja, kusapereka chisamaliro kwa ana pamene amuna ambiri tsopano akupita kukayezetsa DNA chifukwa chokayikira kusakhulupirika kwa akazi awo.
Komabe, chiwerengerochi chikukhudza amuna omwe amapita kukayezetsa DNA okha, makamaka omwe ali kale ndi kukayikira. Izi sizikutanthauza kuti 80% ya abambo onse ku Malawi akulera ana omwe si awo, ayi.
Potsimikizira izi, Kwapata adauzaso The Nation kuti chiwerengerochi ndichosiyana kwambiri ndi chomwe ma bwalo a milandu pa nkhani za m’banja adapeza.
“Milandu yomwe imakafika ku khothi pa nkhani ngati izi, 90% ya abambo imapezeka kuti ndiye abambo eni eni a anawo, ndipo kuti abambo ena amafuna DNA pongofuna kuthawa udindo wopereka chisamaliro cha ana,” Kwapata anatero.

It might might be true but do you believe the machine really do the exact test that bring satisfactory results?