Zaka zitatu kundende pogulitsa nyama yagalu


Nyama Yagalu- Malawi24

Ikakuona litsiro sikata, mkulu uja amkamuzenga mlandu ogulitsa nyama ya galu ku Kasungu, tsopano amugamula kukaseweza jere kwa zaka zitatu.

Bwalo la milandu la Chief Resident Magistrate m’bomali lapeza olakwa mkuluyu emwe dzina lake ndi Juma Fabiano wazaka 49 pa mulandu wogulitsa nyama yagalu.

Izi zichitika ngakhale adayithyola m’maso muli gwaa powuza bwalo la milandu kuti adapha galuyo ngati ndiwo yapakhomo pake osati yogulitsa pofuna kudzipulumutsa.

A Sabiano adawamanga kumapeto amwezi wa June m’mudzi mwa Chisinga powaganizira kuti amagulitsa nyama ya galu ndipo ataonekera kubwaloli koyamba, iwo adaukana mlanduwu.

Juma Sabiano- Malawi24
Sabiano akakhala kundende zaka zitatu

Izi zidapangitsa woweluza mlanduwu, a Chief Resident Magistrate Brian Sambo kuwuza mbali yaboma kubweretsa mboni pa nkhaniyi.

Pofuna kudziteteza, a Sabiano anauza bwaloli kuti anapha galuyo ngati ndiwo yapakhomo osati yogulitsa.

Apa bwaloli lidayika tsiku la pa 12 August mwezi uno ngati tsiku lomwe lidzapereke chigamulo chake.

Bwaloli lapeza a Sabiano wolakwa ponena kuti akhala akugulitsa anthu nyama yagalu.

A Sabiano amachokera m’mudzi mwa Chiuta komwe ku Chiladzulu.

Leave a Reply

Your email address will not be published. Required fields are marked *

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.

Discover more from Malawi24

Subscribe now to keep reading and get access to the full archive.

Continue reading