Pansi mtedza abambo: Imfa pambuyo panu ku maloji


Viagra

“Chonde abambo ngati pali vuto tiyeni tivomereze, apo bii titha ndithu.” Awa ndi ena mwa malangizo omwe avumbwa m’masamba amchezo pomwe chiwerengero cha abambo omwe atsamaya alimkati mwa nkhondo chikumka chikwera.

Chatsitsa dzaye nchoti White Sani, bambo wazaka 48 wochokera m’boma la Zomba, wafa sabata ino ku malo ogona alendo a Ketekete munzinda wa Blantyre komwe adapita kukayankha chirengedwe ndi bwenzi lake.

Lipoti lochokera ku chipatala cha Chiradzulu, likusonyeza kuti Sani wafa chifukwa chakusiya kugwira ntchito kwa mtima wake mosayembekezeka pomwe akuganiziridwa kuti adamwa mankhwala owonjezera mphamvu ku subi.

Sani ndi bambo wachitatu mwezi uno wokha kufa ku loji atamwa mankhwala kapena zakumwa zomwe akuti zimathandiza abambo kuwonjezera mphamvu pomwe akukhalira limodzi ndi achikondi awo.

Sabata yatha, Blessings Nkhuwa wa zaka 30, adapezeka atafa ku loji ina ku Lumbadzi munzinda wa Lilongwe, pomwe akuganiziridwa kuti naye adamwa mankhwala a Kifaru omwe amadzutsa abambo modutsa muyezo.

Kumayambiriro a mwezi uno, Bernado Khinda Chilichawo nayenso adagwa mwadzidzi ndi kufa panthawi yomwe amagonana ndi bwenzi lake ku loji ina m’boma la Dowa.

Chimodzimodzi ndi ena onse, Khinda Chilichawo akuganiziridwa kuti adamwa chakumwa chomwe chinali choti chimuwonjezere mphamvu nthawi yamsangulutsoyo.

Ifazi zadzetsa nkhawa pa kukula kwa mchitidwe ogwiritsa ntchito mankhwala owonjezera mphamvu pogonana pakati pa abambo ndi kukwera kwa chiwerengero cha abambo omwe akufa.

Pakadali pano, m’masamba amchezo ambiri, anthu maka amayi ndi abambo ena omwe amadalira mphamvu za chirengedwe, akulangiza abambo omwe amakonda kugwiritsa mankhwalawa kuti asiye mchitidwewu.

Pakadali pano, anthu pa social media ayankha ndi mantha pa imfazi, ambiri akulimbikitsa amuna kuti asiye kugwiritsa ntchito mankhwala osayesedwa bwino owonjezera mphamvu zogonana.

Ena akuchenjeza kuti kupsinjika kofuna kuwonetsa “umuna” ndi komwe kukukolezera mchitidwe wakumwa mankhwalawa.

Sponsored

Discover more from Malawi24

Subscribe now to keep reading and get access to the full archive.

Continue reading