Mphunzitsi wa time ya Ekhaya, Enos Chatama wati palibepo chifukwa choyankhulira kwambiri chifukwa cholepherana ndi FCB Nyasa Big Bullets.
Poyankhula atatha masewero omwe Ekhaya FC inachokera kumbuyo ndikulepherana ndi Bullets pogoletsana chigoli chimodzi kwa chimodzi mu gawo loyamba la mpikisano wa Airtel Top 8, Chatama anati timu yake inali yaying’ono kwa Bullets ngakhale yakwanitsa kufananitsa mphamvu.
“Ngakhale talepherana, koma Bullets ndi timu yayikulu, tiyipatse ulemu ndipo zotsatirazi sikuti zitipanga kukhala akulu pa Bullets” anatero Chatama poyankhula ndi olemba nkhani. “Kunena kwa ndithe ndithe, Nanthambwe anadzitengera ndiye tisayankhule zambiri, tingobwerera tikakonzekere ndime yachiwiri”.
Mmasewerowa, George Chaomba anatsogoza FCB Nyasa Big Bullets chitangoyamba kumene chigawo chachiwiri, koma Ekhaya FC inadzambatuka ndikubweza kudzera mwa Allen Chihana mkatikati mwachigawochi kuti masewero athere 1 kwa 1.
Chatama anati timu yake inayamba bwino mu mphindi khumi za chigawo choyamba cha masewerowa, koma Bullets inatenga ulamuliro mphindi zinazo.
Iye wati ngakhale chigawo chachiwiri anayamba mofooka pomwe anachinyidwa chigoli cha msanga koma analimbikitsa osewera ake omwe anasewera bwino mpaka kubweza.
“Chigawo chachiwiri tinasewera bwino kwambiri ndipo titabweza tinapitiriza moti tikanathaso kupambana koma sitinagwiritse ntchito mipata yomwe tinapeza”.
Kumbali yake yemwe akugwirizira ngati mphunzitsi wa FCB Nyasa Big Bullets, Heston Munthali anati masewerowa anali ambali zonse.
“Tinasewera bwino mchigawo choyamba chomwe taphonya kwambiri ndipo titagoletsa tinalephere kusunga mipira zomwe zinapangitsa amzathu kuti achite bwino mchigawo chachiwiri” anatero Munthali.
Munthali wati ngakhale zotsatira sizinayende mmene amafunira koma akabwerera akakonza mmene amafooka asanabwere masewero achibwereza.
Ma timu awiriwa adzakumana mu ndime yachiwiri ya ndimeyi, pomwe Ekhaya idzakhale pakwawo, pa bwalo la zamasewero la Mpira mu mzinda wa Blantyre.









