Samalani amayi: Depo akuganiziridwa kuyambitsa mavuto ena mthupi


Depo Provera Meningioma A Rare Brain Tumour Risk Malawi

Jakiseni wakulera wa Depo-Provera, yemwe amayi ambiri kuno ku Malawi amakonda kugwiritsa ntchito, ndipo amapezeka m’zipatala za boma, akuganiziridwa kuti amabweretsa mavuto ena mthupi kuphatikizapo zotupa muubongo komaso kusaona.

Izi zadziwika pomwe amayi ena m’mayiko a United States komaso United Kingdom akasumira kampani yomwe imapanga jakiseniyu ya Pfizer yomweso yakhala ikupanga katemera wa Covid-19 yemwe a Malawi ambiri ndi anthu amayiko ena adagwiritsa ntchito kwambiri nthawi ya mliliwu.

Amayi omwe adasumira kampani ya Pfizer, ati atagwiritsa ntchito nthawi yaitali jakiseniyu, adapezeka ndi vuto la zotupa muubongo. Kupatula zotupazi, anthuwa akuti jakiseni wa Depo-Provera amabweretsaso mavuto a kamvedwe komaso kuona.

Anthuwa akuloza chala kampani ya Pfizer ponena kuti siinapereke chenjezo lokwanira pa mavuto azaumoyo osiyanasiyana omwe jakiseni wa Depo-Provera ali ndikuthekera kobweretsa pa amayi omwe akumugwiritsa ntchito ngati njira yakulera.

Kuwonjezera apo, kafukufuku yemwe adasindikizidwa mu British Medical Journal mu 2024, adapeza kuti kugwiritsa ntchito medroxyprogesterone acetate kwa nthawi yayitali, omwe ndi ena mwa mankhwala omwe amaikidwa mu jakiseni wa Depo-Provera, kumapereka chiopsezo chakuyambika kwa matenda a Meningioma omwe amakhudza chotupa mkati mwa mutu chomwe chimakula m’minofu yozungulira ubongo ndi msana.

Kafukufukuyu adasonyeza kuti matenda a Meningioma si khansa ndipo nthawi zambiri amakula pang’onopang’ono, koma amatha kuyambitsa mavuto aakulu azaumoyo. Zina mwa zizindikiro zake ndi monga kupweteka kwa mutu, khunyu, mavuto a maso, kulephera kumva komanso kuiwala. Nthawi zina, odwala amafunika opaleshoni ya ubongo.

Pakadali pano, kampani ya Pfizer yauza Sky News kuti ikudziwa za chiopsezo chomwe chilipo chifukwa chogwiritsa ntchito mankhwala ena okhala ndi progestogen kwa nthawi yayitali ndipo yati ikuyang’ana mosamala mankhwala ake ena omwe akukhudzidwa komaso kuwachenjeza anthu aku Europe ndi Canada za chiopsezochi.

Izi zikupereka nkhawa kwa amayi m’mayiko a Africa monga Malawi, South Africa, Kenya, Nigeria, Ethiopia, Ghana ndi Zambia komaso ku Asia komwe jakiseniyu akugwiritsidwa ntchito kwambiri, kaamba koti kampaniyi siidafotokoze ngati idayamba kupereka chenjezo pa ziopsezo zomwe mankhwalawa ali nazo pa amayi ogwiritsa ntchito.

Mirandu yokhudza Pfizer ikupitirirabe koma kufika pano palibe khoti lomwe lapereka chigamulo chili chose pa madandaulo omwe amayi ena akupereka.

Join the conversation — share your thoughts on this story

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.

Discover more from Malawi24

Subscribe now to keep reading and get access to the full archive.

Continue reading