Oyimbira watiwonongera masewero – Mkandawire 


Dedza Dynamos- Malawi24

M’mphuzitsi wa timu ya Red Lions, Malumbo Mkandawire, wadandaula kuti kugonja kwake koyamba mu mpikisano wa chaka chino wa FDH Premiership mmanja mwa Karonga United kwadza kamba kakulephera ntchito kwa oyimbira.

Mmene imapita mmasewerowa, panali patadutsa masewero asanu koma osagonja koma lero yachinyitsa kumapeto kwenikweni kuti Karonga United ipambane 1-0.

Mkandawire anati m’masewero onse, oyimbira wakhala akuthandizira Karonga kuti ipambane.

“Aliyense wawona m’mene woyimbira wachitira, sindinena zambiri koma osewera athu nawonso ndi anthu. Ngakhale Karonga yachinya chigoli chabwino koma oyimbira anayesetsa kuti apeze chigoli” anatero Mkandawire.

Red Lions ili pa nambala 7 ndi mapoint okwana 9 pamasewero 6.

Kumbali ya Karonga, chipambano cha lero chomwe adalira chigoli chokhacho cha Godfrey Sibale, chawatengera pa nambala 8 ndi mapoint 8 pamasewero 6.

Zateremu ndiye kuti Karonga United yapambana koyamba pakwawo italephera kutero m’masewero awiri omwe yasewerapo

Join the conversation — share your thoughts on this story

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.

Discover more from Malawi24

Subscribe now to keep reading and get access to the full archive.

Continue reading