Mutu wa Allen Chihana wosewera kutsogolo wa timu ya Ekhaya wasonkhanitsira ma points onse atatu pomwe wawaza yekha timu ya Masters 2-0, kuyitayitsa Masters ma points atatu kachiwiri chiyambireni premiership.
Masewero a mu FDH Bank Premiership lero anafunga pa bwalo la Mpira ku Chiwembe mu mzinda wa Blantyre komwe Masters inali yopepuka pamaso pa Ekhaya.
Mpira ochokera pa kona unakabala chigoli cha Ekhaya pa mphindi ya chi 19 ndipo anyamata a ku Lilongwe anakanika kukonza vuto lolandira mipira mu bokosi kuchokera m’ngodya ndipo anasumbanso Chihana mchigawo chachiwiri kuti zikhale 2-0 pakutha pa mphindi 90 ndi zisanu zowonjezera.
M’phunzitsi wa timu ya Masters, Peter Mponda wati sanganame anyamata ake sanasewere bwino ndipo timu ya Ekhaya inali pamwamba pawo kuyambira pamayambiliro mpaka wenzulo yomaliza.
“Tivomereze kuti anzathu a Ekhaya anali abwino kwambiri kuposa ife pa tsiku la lero, tikapereka zifukwa zogonjera zambiri ndekuti anzathuwa tiwabera shayini,” anatero Mponda.
Mphunzitsi wa Ekhaya Fundi Akidu wati osewera ake apamantha Masters mwa umodzi ndipo wayamika Mulungu chifukwa cha chipambanochi.
Mphunzitsiyu wati anyamata ake analamulira masewerowo ndipo wataindika kuti sakula mutu chifukwa cha chipambano koma kuti ayiwala kaye zomwe zachitika lero ndi kuyang’ana chitsogolo.
Pakutha pa masewero Allen Chihana wakhala osewera wapamwamba m’masewero a msabata ya chisanu ndi chimodzi pakati pa Ekhaya ndi Masters.
Zatelemu Ekhaya ili ndi ma points 10 tsopano mu masewelo asanu ndi amodzi pomwe Masters yatsakamira pa ma points 12.









