
Kunali kukhwekhweleza kwinaku mabuleti ndi ndodo zisakukata pa thupi la womenyera ufulu Sylvester Namiwa. Iye kuyesera kukuwa, “ndithandizeni!” Apolisi oyenera kupeleka chitetezowo amangoyang’ana osachitapo kanthu.
Namiwa amatsogolera zionetsero zomwe gulu la Citizens for Credible Elections (CfCE) linachititsa ku Lilongwe zomwe cholinga chake ndikukakamiza wapampando wa bungwe la Malawi Electoral Commission (MEC) Annabell Mtalimanja komanso Andrew Mpesi kutula pansi maudindo awo.
Koma adakadziwa adakaphika therere! Zionetserozi zinasokonezedwa ndi anyamata adzitho omwe zikwanje zinali waliwali m’manja mwawo kufuna kuchotsa chimbenene anthu omwe amakwanilitsa ufulu wawo opanga zionetsero.
Madzi anachita katondo pa Namiwa pomwe zigandangazi zinatulukira balamanthu ndikuyamba kumubilibinya kwinaku akumukhwekhweleza kufuna kumukokera mu galimoto yopanda nambala yomwe awupanduwa anakwera.
“Akulu akulu, dzikoli lafika pamenepa? A polisi, mukundisiya anthu awa apange nane zimene akufuna? Ndithandizeni!” anadandaula Namiwa pomwe amamenyedwa ndi anyamata azikwanjewa.
Chodabwitsa kwambiri ndi choti izi zimachitika apolisi alipomwepo, koma osamulupumutsa Namiwa ku zigawengazi. Namiwa anapeza mpumulo pomwe apolisiwa m’malo momanga anthuwa, anangophulitsa utsi okhetsa misonzi.
Izi zikuchitika pomwe posachedwapa mkulu wa apolisi m’dziko muno Merlyn Yolamu analonjeza pa mkumano omwe bungwe la Public Affairs Committee (PAC) linachititsaku Blantyre, kuti apolisi agwira ntchito yawo modzipeleka pofuna kuthana ndi mchitidwe wa anyamata azikwanjewa kusokoneza zionetsero.
Pa zionetserozi, galimoto ya mtundu wa lore yomwe imafuna kunyamula woyimba, yaphwanyidwa pomwe galimoto zina zingapo zaphwanyidwa ndi anyamata onyamula zikwanjewa.
Very pathetic