Tsoka likalimba amakuluma ndi wako yemwe! Mwamukumbukira Anthony Bendulo? Nsalamangwe ya ICT, uja anali mboni ya MCP pa mlandu wa zisakho za 2019 uja? Pano akukanditsa posayabwa a Colleen Zamba pomwe akuti mayiwa ndiwo awononga zinthu mu ulamuliro wa a Lazarus Chakwera.
Bendulo akung’alura mosalekeza kudzera pa tsamba lake la fesibuku pomwe mwazina wati Zamba yemwe ndi mlembi wamkulu mu ofesi ya mtsogoleri wa dziko ndi nduna, adapeleka kwa amwenye, mwaulele malo omwe amayenera kukhala a ndalama zokwana K130 biliyoni.
“Mukamadya Nsima Kumeneko Mudziwe Mayi Collen Zamba anapeleka malo a 130 Billion kwa Amwenye Ulele in the name of Investors,” watelo Bendulo pa tsamba lake la fesibuku.
Koma chatsitsa dzaye mchiyani kuti galu alume mbuyake chonchi? Nkhaniyi ikukhudza malo okwana ma hekitala 417 omwe ali ku Area 55 komweso kumatchedwa Magwero munzinda wa Lilongwe.
Malingana ndi Bendulo, Zamba adalamura mwachinyengo kuti malowa apelekedwe mwaulele ku kampani ina ya m’dziko la India yomwe akuti ikufuna kupangapo chitukuko. Iye wati Zamba adachotsetsa ntchito akuluakulu ena a ku Malawi Investment and Trade Centre (MITC) omwe amatsutsana naye pa nkhaniyi.
“Chifukwa chofuna kulondoloza malamulo, Zamba refused to renew CEO’s contract (Paul Kwengwere) nkutumizako Kruger Phiri kukakhala CEO popanda ndondomeko ili yonse (no interview etc) kuti zikatheke zowapatsa malo a company yaku India which also demanded zambili-mbili including Lease ya 99 Years against the 50 years by the Law,” wateloso Bendulo.
Bendulo wadzudzulanso Zamba kuti ndiye wakhala akulakwitsa zinthu zambiri zomwe wati zapangitsa utsogoleri wa a Chakwera pansi pa chipani cha MCP kuwoneka wolephera zedi.
“Mongokumbutsana ine ndi wa MCP Ndipo Boma ndilomweli, koma SPC tikusintha chifukwa uyu wavulaza ntchito zabwino za Apule,” watelo Bendulo.
Chiyambireni kuvumbulutsa zinsisi za Zamba, Bendulo kudzera pa tsamba lake lomwelo wati pali anthu ena omwe akulimbana naye. “Zayambika, kikikiki tima agents taku Dubai kufuna kuoneka dolo ndi ine? Ati kutumiza ka Link koti andipangile hack phone if I click, izizi ndi za kindergarten, za mababy.”
Koma ngakhale zili choncho iye wanenetsa kuti apitilizabe kuvumbulutsa zomwe mayi Zamba akhala akuchita.