Zina ukamva kamba anga mwala ndithu. Pamene okuba mbuzi akutsekeledwa zaka, okuba galimoto akuchoka ku Khoti akusekelela.
Bwalo la majisitileti ku Blantyre lagamula amuna awiri amene anaba galimoto kuti atsatsekeledwe. Ati m’malo mwake asachimwenso basi.
Awiriwo ndi mwana wa mkulu wa bizinesi a Mike Mlombwa ndi mwana wa nduna yakale a Bazuka Mhango. Onse awiriwa ali ndi mayina onga atate awo, amangoonjezelako Junior basi.
Bwalo linauzidwa kuti awiriwa anaba galimoto ya Nissan Tiida ku malo a chisangalalo a Dusk mu boma la Blantyre.
Iwo ati ataba galimotoyo anapezamo zinthu zimene anazigulitsa. Zithunzo anali ma foni a m’manja atatu ndi kompyuta yoyenda nayo, laputopu.
Iwo ati kenako anayamba kufufuza msika wa galimoto limene anabalo. Ati cholinga chawo chinali choti akagulitse zida za galimotolo.
Apolisi ananyengezela kuti ndiwo akufuna kugula galimotolo ndipo awiriwa atalibweletsa ananjatwa ndi kutengeledwa ku bwalo.
Atafika ku bwalo, ogamula anawapeza olakwa ndipo m’malo mowatumiza ku ndende iye anachita za Yesu zowamasula ndi kuwauza asakachimwenso.
Izi zakhumudwitsa a Malawi angapo.
Wachilungamo ndi Allah basi.
Pamenepa kwa ine palibe chachilendo
akakhala pa khate zapheka
Now days money talk 4everything
Chilichonse chalowa DPP
Bosses never go wrong, mark my words
try owez try not to be a poor man…odi ndisiye kuwerenga izi nkapange zoti ndisakhale poor
where is the prosecution authority,the judgement of this case should have been appealed
Amabungwe Ali Ziiii Osanenapo Kanthu Alandila Mamanja Anthu Oyipa Inu Nkhani Ya Cash get Mukulephela Kumugwila Joice Banda Bakili Angonjoya , Chaponda Angonjoya Anthu Okuba Inu Lero Mwatibwelesela Chiphaso Mukuti Tizilipira Pachaka Muzakhutisidwa Liti? Bolaso Ku Iguputo Kokuja
Panopa zikulankhula ndi Ndalama osati anthu.
Ndende anamangila amphawi kuba mbuzi uli mmadzi zaka 10 Ku ndende kkkk
Apa sizinayende bwino. Chilungamo palibe. Ndiye chifukwa chache anthu akagwira wakuba amangopheratu. Amaopa nyansi ngati izi. Kuli anthu ambili ku chichi, maula ndi ndende zina omwe mwina anaba half bag ya chimanga nkugwidwa. Awa anawa amayenera akasewenze ku ndende. Ngati sapita ku ndende pakhala povuta kuti ma khoti atumize ankuba ena ku ndende pomwe akuba ena akhululukidwa. Kodi judge ameneyu sukulu anakaphunzila kuti?
OKUBA
Ifvyou can’t beat them join them; nkhani apa pangani ndalama and you will join the elite! Osamangoti God will intervene this that while anzanu ndalama is intervening! Inu ntchito kumati ndadya bebi yakuti yakuti! Mumva painz
Ndalama zimayankha ngakhale utakhala ndi mulandu oopsya motani Koma uli ndi ndalama .sungaseve ndende.
Mwana wa ndani?
Ndiye kuti wakhala pa nkhate ameneyo
Zonse kungosiya mmanja mwa mulungu
Judge walandira zingati? Chilungamo palibepo apa. A police akugwira ntchito modzipereka ndipo akupangidwa ulesi ndi oweluza milandu makape amenewa. Thandizani okubawo apolisi akamubere yake galimoto judge ameneyo ndi opusa
Tell the judge to be more careful death at door step.
ndkufuna ndisamuse munda wanga upite kulimbe coz mvula ikugwako heve…
Olemera salakwa ngati alakwa it’s always by mistake.
Liyanja achuma dziko
Ali CHAVURA zaka ten
Galu sayenda ndi mbuzi ayi koma boma ili
Osauka angatani pa maso pa achuma
Limenelo ndiye dziko
Koma musiyeninso oyimba uja
Asiyeni adzikondera choncho koma court lakumwamba, ndilomwe lidzagamule milandu ya winaaliyense mwachilungamo. Dziko, limakondera koma boma lakumwamba, sipadzakhala zimenezo osauka alibe mphamvu yowapulumutsa m’manja mwaoweruza achinyengo.
I always say our judges and magistrates are very corrupt,this is a simple example,,corruption at its best.By the way what’s the name of the magistrate.
Ali mayiko ena, the state could have appealed the judgement. This is very unfair to those who are in prison or have been there for stealing a stainless razor blade.
Osadabwa akuba okhaokha atulutsana
Inch yawajinga hiyo
Ali mayiko ena, the state could have appealed the judgement. Paja Mlombwa snr anagula fridge K4 million pa Blue night fundraising chaka chinacho.
Mulungu akungoyang’na kma tsiku lina adzakutoperani,mungonditurutsira Chavura wangayo
ndende ndi zawathu osauka but everything God amaona.znalembedwa kale
The magistrate must be investigated!!!
Muthu Olezela Ofuna Kulandila Envilop Kwapulent Kundende Pomwe Uyu Zokoza Kuba Galimoto Kumutaya Aaa Malawi Choona Chili Pati?
kma chavura. mukumusunga ku police jst bcz of song. mbava kukhululukiridwa shame on u, akukanthani mulungu n ma drought avutawa it’s because of ur injustice n immorality
bayanya shem
Zikomela achuma
Be reminded bro that Prisons were built for poor people, just mark my word.
zitsiru za anthu God will punish them
Uku ndiye kulimbikitsa umbava ndi umbanda chifukwa mosazindikira kanthu mwina sakudziwa kuti zija tikuwona zomatsomphora apresident envelope zija zifukwa zina ndi momwe akuchita amakhoti akamapeleka zigamulo zosakhala bwino ngati izi Chonchi palibe angasiye mchitidwe wokuba
setting very bad precedent…
Wins kupanga compose nyimbo akukanika kumpasa bail,wokuba zinthu zama million osatsekeledwa kundende,Malawi wanga ukupita kuti nanuso amabungwe simmatithandiza you are just sitting and seeing.Malawi is full of corruption. Shithole country as Trump said.
Alibe mawu
Zopusa zokhazokha izi. Dziko likamakhla lopanda ndondomeko vuto limakhala limenelo
Mulungu akanati azigulisa mvula eeee enafe minda yathu itauma kalekale chifukwa chinyengo chameratu mizu pa nyasaland pano
Yemwe walamula kuti mlandu watha iyeso ndiwakuba.kukhala Mwana wanga kumulamura dzaka dzisanu,koma poti ndimwana wamuthu ochita bwino ndichifukwa waturuka.Komaso Athu akamati kunja kuno kuli Mankhwala mukhulupilire,palikathu.And ineyo ndimakhulupirila kuti pali makhwara amatulusa muthu roko atapha muthu dzake amatuluka.
Life!
While Mwiza is still under police custody God punish them
ok tikuonan very soon
Mulungu si munthu
chavura sanabe kathu kapena kuononga pena pake koma akutsekelabe mpaka pano wina kuba galimoto akut amukhulukila hahaha
Ndikuziwa osauka paziko lampansi pano chawo palibe malipilo athu alikumwamba
2 Corinthians 8:9.
kumwambaso kulib chathu bra.
Kkkkkkkkkkkkkkkklkk koma mcs
Ngati osawuka sitichita bwino pasi pano kumwamba kuliso mavuto kkkkkkkk
Mm koma mwini wakeyo azawona mopangila kkkkkkkkkkkkkkk
Nchifukwa chake ndimadana ndi kusauka. Ukakhala osauka ndithu ukhoza kuuzidwa ukolope mu chimbuzi ndi Lilime.chifukwa chofuna ndalama kukolopa ndithu nanga upanga bwanji?
Wina akutsekeledwa chifukwa cha music
ndi zosadabwitsa
koma chavula mkumangidwa. ..bullshit #panopa #free_chavulat